Pulogalamu ya ECRP yatha

Pulogalamu yophunzitsa anthu kuteteza chilengedwe ya Enhancing Community Resilience Programme (ECRP) yatha itakhalapo zaka 6 ikuphunzitsa anthu m’maboma 7.

Mkulu woyendetsa pologalamuyi, Sophie Makoloma wati ndi wokondwa kuti m’zaka 6 zomwe akhala akuphunzitsa anthu, dziko la Malawi ndilosinthika. Maboma omwe apindula ndi Nsanje, Chikwawa, Mulanje, Thyolo, Mwanza, Machinga ndi Kasungu.

Kheli pano ali ndi ziweto,kuphatikizapo mbuzi

“Ndine wa chimwemwe kuti anthu akudziwa chochita kuti azembe ngozi zachilengedwe komanso akukwanitsa kusunga ndalama. Akutha kupanga mapulogalamu osiyanasiyana kuti chilengedwe chisamalike,” adatero Makoloma.

Kutseka pulogalamuyo kudachitika Lachitatu m’sabatayi pamene akuluakulu apulogalamuyo adakumana mumzinda wa Blantyre.

Pulogalamuyi imaphunzitsanso anthu momwe angachitire kuti asakhudzidwe ndi kusefukira kwa madzi komanso momwe angathanirane ndi kusintha kwa nyengo.

Zina zomwe anthuwa amaphunzitsidwa ndi monga kugwiritsa ntchito mbaula zamakono, ulimi wa mthirira, ulimi wa kasakaniza, kusunga ndi kubwereketsa ndalama, kubzala mitengo komanso kuweta ziweto.

Malinga ndi Makoloma, pulogalamuyi idacharira kuti ipindulitse anthu 177 000 koma pakutha pa ndime, anthu oposa 1.5 miliyoni ndiwo akumwemwetera kuti zawo zayera.

“Pamene tikutseka pologalamuyi, tikunena kuti tagwiritsa ntchito pafupifupi K15 biliyoni]. Komatu ndasangalala kuti zomwe timafuna zatheka,” adatero Makoloma.

Woyang’anira polojekitiyi koma akugwira ntchito ku Churches Action in Relief and Development (Card) m’boma la Thyolo, Chifundo Macheka akuti anthu a m’bomalo zawo zayera.

“Anthu akutha kubwereka ndi kubwereketsa ndalama. Ulimi ndiye simungachite kufunsa komanso anthu akuweta mbuzi kudzera m’polojekitiyi,” adatero Macheka.

Mabungwe a Department for International Development (DfID), Irish Aid ndi Norwegian Embassy ndiwo amathandiza ndi ndalama.

Mlimi mmodzi amene wathandizika ndi pologalamuyi, James Kheli wa m’mudzi mwa Sudala kwa Senior Chief Kanduku m’boma la Mwanza wati zake zidayenda ndipo palibe kubwerera mmbuyo.

Kheli ali ndi mbuzi 10, wayamba kukolola matumba 50 a chimanga kuchoka pa 15. Iye ndi banja lake abzala mitengo 300; akupanga ulimi wa mleranthaka komanso ali ndi munda wa chinangwa momwe akupha ndalama.

“Ndikulipirira mwana wa Folomu 4, pa telemu ndi K20 000. Ndamanga nyumba ya malata, ndagula wailesi komanso mpando wapamwamba,” adatero Kheli.

Share This Post