Nkhani

Umhlangano wa Maseko Ngoni lero

Listen to this article

 

Kutentha masanawa kumanda kwa Gomani kwa Nkolimbo m’boma la Ntcheu pamene Angoni a m’maiko monga Zambia, Mozambique, Tanzania, South Africa komanso Swaziland akhale akukumana pamwambo wachikhalidwe.

Umhlangano ndi mwambo wa Angoni umene pamakhala magule komanso miyambo ina monga kuulutsa nkhunda yoyera ndi kukhwisula.gomani

Inkosi ya Makhosi Gomani Wachisanu pocheza ndi Tamvani lachitatu yati zokonzekera zonse zatheka kuti mwambowu uchitike lero ndipo anthu ochokera m’madera ena adayamba kufika kumaloku Lachiwiri.

Pamwambo wokhwisula anthu amasonkhana mmawa ndipo amakayendera pamene adagona Chikuse Gomani l. Chikuse ndiye mfumu yoyamba ya Angoni a kwa Maseko imene idaphedwa ndi azungu chifukwa chomenyera ufulu wa anthu akuda.

Pamandapo pamakhala mapemphero komanso mwambo wopempha madalitso ndipo mfumu yaikulu ya Angoni a kwa Maseko ndiyo imatsogolera mwambowo.

“Apapa ndiye kuti wotsogolera mwambowu ndineyo. Pamwambowu amayi samakhalapo. Mwambo umenewu ndiwo umayambirira kuchitika ndipo uchitika nthawi ikamati 5 koloko mmawa,” adatero Gomani V.

Iye adati pamwambowu pakakhalanso mwambo woulutsa nkhunda zoyera.

“Kuulutsa nkhunda kumatanthauza mtendere. Angoni timalimbikitsa mtendere ndiye pamwambowu timaulutsa nkhunda zoyera zomwe [zikuimira] mtendere,” adaonjeza.

Mwambo wa chaka chino wakumana ndi zovuta zingapo monga kumwalira kwa Inkosi Phambala komanso Bvumbwe.

Gomani adati iyi ndi nkhani yachisoni ndipo pakakhalanso nthawi yokumbukira mafumuwa, omwe adati  adali mafumu okonda ndi olimbikitsa chitukuko m’madera awo.

Zovala ndi zakudya Zachingoni ziyalidwa kuti anthu akasirire komanso kugula. Gomani adatinso ngakhale mwambowu ndi Wachingoni, anthu amitundu yonse akuitanidwa kuti adzasangalale nawo limodzi.

Ngoma, uyeni, nkhwendo ndi msindo ndi ena mwa magule amene asangalatse anthu obwera kumwambowu, adatero Gomani.

Related Articles

Back to top button
Translate »