Chichewa

Wopezeka’ ndi yunifomu ya polisi anjatidwa

Listen to this article

 

Apolisi ku Zomba akusunga m’chitolokosi bambo wa zaka 25 pomuganizira mlandu wopezeka ndi yunifomu ya polisi komanso mfuti popanda chilolezo.

Nyaude: Tidadabwa ndi zochitika zake
Nyaude: Tidadabwa ndi zochitika zake

Mneneri wa polisi kuchigawo chakummawa, Thomeck Nyaude, watsimikizira za nkhaniyi ponena kuti adanjata Clement Mawerenga wa m’mudzi mwa Katete, T/A Malemia pamsika wa Songani.

“Tidadabwa ndi zochitika za mkuluyu ndipo titamuyandikira tidaona kuti sadali wapolisi ngakhale adapezeka ndi katunduyo. Adali ndi malaya komanso mabuluku a polisi 12 kuphatikizapo mfuti,” adatero Nyaude.

Kuchigawo chakummawa komweko, apolisi m’boma la Machinga atsekera amuna anayi powaganizira mlandu woba katundu wa K3.7 miliyoni.

Nyaude adati anthuwa akuwaganizira kuti adaba mapaipi 244 a madzi ndi zipangizo zina kwa White Mbalame, wa m’mudzi mwa Kawinga, kwa T/A Kawinga m’bomalo.

Nyaude adati amene akuwaganizira za mlanduwu ndi Madalitso Wasi, Andrew Amin, White Samson ndi Christopher Chapita.

“Tikuwaganizira kuti adapalamula mlanduwu mu November 2013. Titangowamanga, tapeza mapaipi 160,” adatero mneneriyu.

Oganiziridwawa onse akuchokera kwa T/A Mlomba m’bomalo.n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »