Nkhani

Adandaula za nyumba ya chisoni

Anthu okhala m’dera la Lisungwi m’boma la Neno adandaula ndi kusagwira ntchito kwa nyumba ya chisoni.

Nyumba ya chisoni ya pa chipatalapo yakhala isakugwira ntchito kwa chaka chimodzi ndi miyezi ingapo tsopano ndipo anthu kumeneko akukakamizidwa kutengera matupi a abale awo ku nyumba za chisoni ku Mlambe m’boma la Blantyre ngakhalenso ku chipatala cha boma la Mwanza.

Chipatala cha Lisungwi. I Joseph Mkango

Malinga ndi mmodzi mwa anthu okhudzidwa, yemwe adapempha kuti tisamutchule dzina, kusowa kwa nyumba yachisoni kukuchititsa kuti abale ena asamakhale nawo pa maliro chifukwa akumaika msanga.

“Maliro akangochitika, achipatala akumauza anthu kuti anyamule thupilo ndi kukaika kwawo. Kuika msanga maliro kukuchititsa kuti abale akutali asakhale nawo pa mwambo wa maliro. Zikutiphwanyira chikhalidwe chathu,” adatero iwo.

Mkuluyo wati ngakhale mmbuyomo amangoona izi zikuchitikira anthu oyandikana nawo, pa 18 June zidachitika pa khomo pake.

“N’zovuta koma musanditchule. Ife zitatigwera pa 18 June tidali wokakamizika kutengera thupi la malemu bambo anga ku Mlambe tisanapite nawo kwathu kwa Bvumbwe ku Thyolo. Akadatithandiza,” adatero iwo.

Atamwalira bambo awo, mkulu winanso ndi abale awo adakakamizika kukaika bambo awo ku Zalewa asadauze abale awo mokwanira za imfayo.

“Munthu akamwalira ku wodi, akumangopita ku nyumba ya chisoniyo monga mmene zimakhalira koma palibe chimene chikuchitika kumeneko. Ngakhale kukonza maliro kulibe,” adatero iwo.

Ndipo akulu enanso ati kusagwira ntchito kwa nyumba ya chisoni kukulowa anthu m’thumba polingalira kuti akumatengera matupi a abale kuchipatala cha Mlambe kapena Mwanza.

“Munthu waferedwa, tsono mayendedwe kupita ku Mlambe n’kudzabwereranso ku Neno ndi ndalama zambiri. Zikutipweteka zimenezi,” atero iwo.

Koma mneneri wa za umoyo m’bomalo Mayi Carlo Banda, wati mavuto omwe otaya okondedwa awo akhala akukumana nawo akhala mbiri yakale posachedwapa.

Iwo ati kusagwira ntchito kwa nyumba ya chisoniyo kumachititsa ogwira ntchito pachipatalachi  kuti asamasunge matupi a anthu m’chipindachi kwa nthawi yaitali ndipo amalangiza anamfedwa kuti azitenga matupi a abale awo mwachangu poopa kuti angaonongeke.

“Vutoli litha posachedwa chifukwa padakalipano amisiri ali kalikiliki kukonza makinawa pamene madongosolo ogula makina ena atsopano alimkati pofuna kuthetseratu vutoli,” adatero a Banda.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button