Kandideti walonjeza nsapato, maendedwe otsika mtengo
Malonjezo pa nthawi ya chisankho si achilendo. Koma pali ena oti ukamva, umagwedeza mutu.
Yemwe adzaimire chipani cha UTM ku dera la kum’mwera m’boma la Nsanje ngati phungu a Bester Chiungano ati akadzapambana pa chisankho chikubwerachi, adzagulira nsapato komanso kulipilira fizi ana omwe adzasankhidwe kupita ku sekondale. Iwo anati adzaperekanso mayendedwe otsika.

Polankhula Lachiwiri pa mtsutso omwe bungwe linachititsa ku deralo, iwo anati cholinga chawo n’kuchepetsa mavuto omwe anthu akukumana nawo ku deralo.
Pa nkhani yotsitsa mitengo ya mayendedwe, a Chiungano anati adzagula ma Coaster angapo omwe azidzayenda pakati pa Marka ndi Blantyre ndipo anthu azidzalipira motsika mtengo.
“Ndidzalipilira fizi onse omwe asankhidwa kupita ku sekondale ndi kugulira nsapato wina aliyense. Ndidzagula ma coaster ndipo anthu azidzilipira K10 000 kupita ku Blantyre kuchokera ku Marka ulendo womwe panopo akulipira K25 000,” iwo anatero.
A Chiungamo anapitiliza kunena kuti adzaonesetsa kuti mabokosi a maliro adzikonzedwa malo wochuluka m’deralo komanso kudzakhale mijigo komanso sukulu zambiri.
Koma katswiri pa ndale a Ernest Thindwa anati akukaika ngati a Chiungano angadzakwanilitse zomwe alonjeza.
“Takhala tikumva malonjezo ambiri kuchokera kwa anthu a ndale. Nthawi zina timadabwa n’kumadzifunsa kuti koma zimenezi zingatheke? Choncho zomwe analonjeza a Chiungamo n’zokaikitsa,” iwo anatero.
A Thindwa anati akumvetsa chimene anthuwa amapereka malonjezo chifukwa akugwira ntchito zomwe sizawo.
“Ntchito ya phungu sikumapereka zinthu, koma kukapanga malamulo ku Nyumba ya Malamulo, kuunika momwe boma likuyendetsera ndalama komanso ngati likutsata malamulo. N’zachisoni kuti zonsezi azisiya,” iwo anatero.
Katswiriyu anati khalidwe lolonjeza likupitilira chifukwa Amalawi sakuonetsa kukwiya. Iwo anapereka chitsanzo cha malonjezo omwe anaperekedwa m’mbuyo koma sanakwanilitsidwe.
“Amalawi ali ndi mkwiyo koma sakuuonetsa. Ayenera kuuonetsa kuti andale ena atengerepo phunziro n’kumachita mantha,” anatero a Thindwa.
Ku mtsutsoko kunalinso yemwe anali phungu ku derail a Ramzan Juma Mahomedi omwe apikisana nawonso ulendo uno.
Iwo analonjeza kuti apitiriza pomwe anasiyira.
“Ndakhala ndikupanga zitukuko zambiri ku dera lino ndipo ndipitiriza kutero. Cholinga changa n’kuonesetsa kuti zitukuko zafalikira ku dera lino kudzera ku thumba la chitukuko la Constituency Development Fund,” iwo anatero.
Mkulu woona ntchito za bungwe la Women’s Legal Resources Centre (Wolrec) a Ireen Ntonga anapempha anthu kuti adzasankhe mwanzeru osati chifukwa choti alandira ndalama kapena katundu.
Iwo anati malamulo woyendetsera ndale m’dziko lino salola kuti munthu kapena zipani adzipereka ndalama kupatula nsalu za makaka a zipanizo.
Mkulu woona ntchito za bungwe la Malawi Electoral Commission ku derali a Monica Chimombo anapempha anthu kuti azipita ku misonkhano ya ndale yosiyanasiyana n’cholinga choti azasankhe anthu a mfundo zabwino pa chisankho chikubwerachi.
Iwo anatero: “Ndipemphe mafumu, aphunzitsi ndi akuluakulu ena kuti azipereka mwayi wofanana kwa andale ngati akufuna kuchititsa misonkhano.
“Ndipemphenso achinyamata kuti apewe kugwiritsidwa ntchito ndi andale kusokoneza misonkhano kapena komachotsa mbendera za ena.
Mtsutsowu unakonzedwa ndi mabungwe a Wolrec, Oxfam in Malawi, National Initiative for Civic Education (Nice) ndi khonsolo laboma la Nsanje ndi thandizo lochokera ku European Union.



