Nkhani

Kandideti wa MCP wapambana anthu asanavote

Bungwe la zachisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati yemwe amaimira chipani cha Malawi Congress Party (MCP) ku dera la Lilongwe Chilobwe a Lawrence Chaziya apambana ngati phungu wa deralo ngakhale chisankho chisanachitike.

Wapampando wa MEC a Annabel Mtalimanja ati a Chaziya apambana kaamba koti anali okhawo omwe anaonetsa chidwi kuima ngati phungu wa delaro.

Lawrence Chaziya

“Choncho bungwe la MEC likulengeza kuti a Lawrence Chaziya asankhidwa kukhala phungu wa ku Nyumba ya Malamulo wa dera la Lilongwe Constituency mopanda kupikisana,” iwo anatero.

Gawo 45 la malamulo okhudza pulezidenti, phungu ndi khansala amapereka mphamvu ku bungwe la MEC kulengeza kuti munthu wapambana pa chisankho ngati palibe opikisana naye.

Mneneri wa MEC a Sangwani Mwafulirwa anati chifukwa cha ichi, bungwe lawo silichititsa chisankho cha phungu.

 Mneneri wa MCP a Jessie Kabwila anati izi zikusonyeza kuti chipanicho n’champhamvu pamene akukonzekera chisankho cha pa September 16.

“Zipani zina sizinaonetse chidwi chopikisana nawo ku derali chifukwa chimadziwa kuti chipani cha MCP n’champhamvu komanso chichititsa kuti chidzachite bwino pa chisankho.”

 A Chaziya sanayankhe mafunso komanso foni.

Bungwe la MEC linalandira kalata za anthu omwe adzapikisane nawo pa chisankho cha pa September 16 kuyambira pa July 24  mpaka July 30.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button