‘Ikutrenda’ ndi Scorchers
Timu ya mpira wa miyendo ya atsikana ya Scorchers yagwedeza masamba a mchezo, inde kutrenda, pomwe yagometsa ambiri polowa mpikisano wa maswerowa muno mu Africa mpaka kufika ndime yomaliza.
Timuyi lero ikumenya ndime yomaliza ndi timu ya Cameroon m’dziko la Morocco ndipo akapambana apeza $1 miliyoni koma akagonja abwera kuno ku mudzi ndi $750 000.

Zonsezo zili apo, iwowa popeza adafika semifainolo, adadzigulira tikiti kukamenya ku mpikisano wa dziko lonse umene udzachitikire ku Brazil chaka cha mawa.
Popeza timuyi yachita zozizwitsa, asangalatsi a m’masamba a mchezo, ma content creator akuyesetsa kuti penapake atchulepo Malawi cholinga apeze ma like ndi ma comment kuti zawo za monetisation (kupeza ndalama popeza anthu ambiri pa tsamba la mchezo) ziyende.
Timu imene amasewera Temwa Chawinga m’dziko la America ya KC Current nayo yakhala ikuponya ma post a Chichewa kumuchemerera. Izi zadza pomwe Amalawi achita follow tsamba la mchezo la timuyo, mpaka kufikitsa pa 1 miliyoni.
Tsiku lina idangoti: Nanga tingalime? Linalo imvekere: Scorchers imadoda da-da-da.
Ngakhale nyumba yokhazikika youlutsa mawu ku Mangalande ya BBC News Africa Lachisanu mpaka idaponya Chichewa pa tsamba lake ikutambasula za kudabwitsa kwa Malawi: “Tikutenga chinthuchi Malawi?”
Nthawi zambiri, ma comment a tsambalo saposa 200 koma kungotero, adagunda 4 000.
Ma content creator ndiye osanena. Doctall Kingsley, wa ku Nigeria, waitengera pena ndipo akuphunzitsa ngakhale Chichewa komanso kunena za malo ochititsa chidwi a ku Malawi. Ma comments akumafika 12K koma kutchula maiko ena a mu Africa.
Ngakhale oimba a ku Zambia a Organized Family nkhaniyi aitengera pena, pomwe iwo akulimbikira kuti dziko lawo ndi Malawi ndi limodzi: Malambia.
Ndipo wina wotchedwa Football Banterz posakhalitsapo amapeza ma comments osaposa 200 koma kungonena kuti Malawi ikangochinya Algeria iye adzasamba akujambulidwa ndemanga zinafika 18K.
Naye Morisson Sports wa ku Nigeria adachilimika kuti akufuna passport ya ku Malawi. Naye Daniel Obasi adachilimika kuchemerera Temwa ndi Tabitha.
Funso n’kumati pomwe zafikapa, ma content creator a ku Malawi angatani kuti azipindula ndi ndalama momwe akunja akuchitira, kutchukira pa Malawi.
A Victor Daffrece, yemwe ndi muulitsi wa Face to Face Podcast adati pakadali zovuta zina kuti Amalawi ayambe kupindula pokhala ma content creator.
“Ntchito ikadalipo chifukwa mwezi wa April, a Meta omwe adalumikizana ndi a Macra adachititsa maphunziro a zomwe zikuyenera kuchitika kuti phindu liyambe kuoneka,” adatero iwo.
Zonse zili mfumu ya mzinda wa Blantyre Jomo Osman omwe ali ku Rabat m’dziko la Morocco Lachisanu adati ‘morale ili high’ ndipo likululo layaka moto.
“Tikuwalandira onse amene akubwera m’dziko muno kudzaipatsa moto Scorchers ndipo chinthuchi tikutenga. Amalawi akonzeke kudzatilandira pomwe tikubwera nacho. Anthu aona red kuti tiwachemerere,” watero iye.
Mkulu wa National Bank of Malawi (NBM) plc adati banki yawo imene ndi sponsor wa Scorchers ndi yonyadira kuti timuyo yafika ndime yomaliza ndipo adathokoza bungwe loyendetsa mpira wa miyendo la FAM ndi loyendetsa mpira wa miyendo ya amayi la NWFA kaamba ka ntchito zimene agwira.



