Alangiza aphungu achepetse tulo
Aphungu a ku Nyumba ya Malamulo adakwangula mkumano wawo sabata yatha atadutsitsa mabilu 14 omwe ambiri akukhudza za chuma ndi momwe ndalama za Amalawi zingatetezeredwe.
Koma atsogoleri a nyumbayo ati sikuti momwe mkumanowo watha ndiye kuti aphungu azigona chifukwa zomwe adakambirana pa mkumanowo n’zoyenera kulondolozedwa.

Sipikala wa nyumbayo a Sameer Suleman adalangiza aphunguwo kuti akabwerera kwawo akaonetse kuti ku Nyumba ya Malamulo kumachitika zakupsa.
“Tidali ndi mkumano waphindu kwambiri koma tikabwerera n’kumakangogona, zonse zomwe tidakambirana n’kumanga kuno zidzakhala za chabe,” adatero a Suleman.
Mtsogoleri wa nyumbayo a Jappie Mhango adayamikira aphunguwo poonetsa chidwi pa zokambirana zonse ndipo nawo adalangiza aphunguwo asakafooke koma azikaunikira momwe zinthu zikuyenera kuyendera.
“Tisakaiwale udindo wathu woyambirira wounikira momwe zinthu zikuyenera kuyendera. Zonse zomwe zidachitika muno pomwe timakumana n’zaphindu ku dziko ndiye tikaonetse kufunikirako tikapita,” adatero iwo.
Mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma a Simplex Chithyola Banda adati Amalawi akaweruza aphungu awo potengera ntchito zawo osati kudutsitsa mabilu.
“Ena aunikira kale kuti ntchito yeniyeni ili ku madera kwathu ndiye tikapita tikuyenera kukasonyeza kuti timadziwa chomwe tidalowera m’Nyumba ya Malamulo,” adatero a Chithyola Banda.
Koma ngakhale aphunguwo adakwangula mkumano wawo atadutsitsa mabilu ofunikirawo, Amalawi sadakhutire kuti nkhani zina zikuluzikulu monga lipoti la hotela ya Amaryllis.
Aphunguwo asadayambe mkumano wawo, wapampando wa komiti yomwe ikufufuza za hotelayo a Steven Malondera adalonjeza kuti lipoti la kafukufukuyo liperekedwa m’nyumbayo.
Wapampando wa mabungwe olimbana ndi katangale la National Anti-corruption Alliance a Michael Kaiyatsa ati lipotilo likuyenera kutuluka kuti za mkati zidziwike.
“Amalawi adikira kokwana ndipo tsopano tiyamba kuganiza kuti pali chomwe akubisa. N’kale lomwe kafukufukuyo adayamba ndipo kufika pano amayenera kutha,” adatero a Kaiyatsa.
Mkumanowo adauonjezera ndi sabata imodzi pofuna kupereka nthawi yoti nyumbayo ikambirane mabilu onse ndi nkhani zina zomwe boma lidakonza.



