Bokosi si chitukuko
Mafumu ena m’dziko muno apempha aphungu a ku Nyumba ya Malamulo kuti asiye kugula mabokosi pa maliro ponena kuti bokosi la maliro si chitukuko.
Mafumuwa ati izi zikulimbikitsa kuti anthu azikhala akudalira kalikonse kuchoka kwa aphungu zomwe zimachititsa kuti aphunguwo asiye kulunjika pa nsanja zokweza dziko lino ku nkhani ya chitukuko.
Malingana ndi a Gulupu Onga, a m’boma la Chiradzulu, si kuti mafumuwa akudana ndi khalidwe lofuna kuthandiza lomwe aphunguwa amakhala nalo, koma nthawi zina zimasokoneza nzika kuzindikira udindo omwe aphungu ali nawo pa mapeto pake zimakhudza chitukuko cha ku dera.
“Tikuthokoza kuti aphungu amakhala ndi mtima wofuna kuthandiza koma pakufunika kuika ndondomeko zoyenera kuti zizitsatidwa pofuna kuthandiza ku mbali ya bokosi. Kodi bokosi ndi chitukuko?” adafunsa iwo.
A Onga adatinso ndi wodabwa kuti ngakhale mabanja ena amaoneka kuti kuthekera ali nako, koma zovuta zikagwa monga zokhudza maliro amapitabe kukapempha kwa phungu wa ku dera kuti awathandize ndi bokosi
Malingana ndi mayi Alinane Bokosi a m’mudzi mwa gulupu Mbalame ati kugula bokosi pa maliro si chitukuko.
“Tikasankha munthu timafuna atitumikire ku zitukuko zosintha moyo wa munthu monga kumbali ya madzi abwino, misewu, sukulu, misika, zipatala ndi zina zambiri. Munthu sungathandize mtembo chifukwa umafunika kuthandiza anthu omwe ali moyo,” adatero iwo.
Senior Chief Chapananga ya m’boma la Chikwawa adagwirizana ndi a gulupu Onga kuti si ntchito ya aphungu kugula bokosi.
“Aphungu akuyenera azigula mabokosi mwa kufuna kwawo komanso osati chikhale chizolowezi chifukwa si ntchito yomwe tidawasankhira pa udindowo,” adatero iwo.
Koma Senior Chief Mkumpha a m’boma la Likoma ayamikira aphungu omwe akupitiriza kugwira ntchito za chifundo ponena kuti ndi gawo limodzi lofuna kuthokoza anthu a ku dera powasankha.
“Aphunguwa amatithandiza mu zambiri nkhani za mabokosi zili apo choncho sikoyenera kuti asiye kuthandiza chifukwa ngati angasiye ndiye kuti angavutike kwambiri ndi anthu athu,” adatero iwo.
A Mkumpha adapitirira kuyamikira utsogoleri wapano kaamba kounikiranso thumba la chitukuko cha CDF kuti chizikhala manja mwa makhansala ponena kuti izi zithandizila kuti Amalawi amvetsetse bwino udindo wa aphungu komanso kukhutira pa ndalama za m’thumba mwawo zomwe aphunguwa amatenga ndi kugwiritsa ntchito.
“Zoona, poyamba aphungu amagwirisa ntchito ndalama za CDF n’kumanama kuti ndi zawo koma pano ndi pomwe tizikhulupirira kuti phungu wagwiritsadi ntchito ndalama yake,” adaonjezera iwo.
Pothirapo mlomo, katswiri pankhani za ulamuliro wabwino a Augustine Magolowondo adati ndi wokondwa kuti mafumu tsopano ayamba kuzindikira udindo omwe ali nawo ndi kuyamba ntchito yolimbikitsa ulamuliro wabwino.
“Choyamba tikuyenera kuvomereza kuti umphawi ndi omwe umapangitsa anthu kuti akapemphe bokosi chifukwa iwo sangafikire mtengo wake, chopweteka chimakhala kuti ndalama zogulira bokosi zimapezeka pomwe mu zipatala mukusowa zipangizo zoyenera monga mankhwala omwe akadatha kupulumutsa miyoyo,” adatero iwo.
A Magolowondo adaonjezera kuti pakufunika kuunikanso bwino ndale za dziko lino pofuna kuthana ndi khalidwe lodalira kuti andale ndiwo ali ndi mayankho a mavuto onse.



