Nkhani

Mikunzi ya DPP yaombana mitu

Mikunzi iwiri ya Democratic Progressive Party (DPP) yautsirana chenjelere pa nkhani ya ziphuphu m’boma.

A Sipikala a Nyumba ya Malamulo a Sameer Suleman adauza Asilamu pa mzikiti wa ku Area 13 ku Lilongwe kuti ziphuphu zidamanga nthenje m’boma moti n’kovuta kuti atsogoleri athane nazo.

A Suleman akufuna kuchepetsa ziphuphu. I Nation

A Suleman, omwe ndi phungu wa DPP wa m’dera la Blantyre-BCA-Chigumula, adati kuthana ndi ziphuphu kufunika kusintha dongosolo ndi ndondomeko zina zoyendetsera zinthu m’boma.

“Ngakhale mtsogoleri atakhala wabwino motani, sangakwanitse kuthana ndi ziphuphu chifukwa cha ndondomeko zomwe zimatsatidwa padakali pano,” iwo adatero.

Mawu awa sadakondweretse akuluakulu ena a boma ndipo nduna yofalitsa nkhani a Shadric Namalomba adalemba patsamba kale la mchezo la Facebook kuti Sipikayo apereke umboni wa ziphuphu zomwe zikuchitika m’boma pasadathe masiku 7.

Iwo adati Nyumba ya Malamulo ilibe mphamvu yofufuza ziphuphu kaamba koti ntchito imeneyo ndi ya apolisi, msungichuma wamkulu wa boma, komanso bungwe la Anti-Corruption Bureau.

Koma a Suleman adafunsa: Kodi a Namalomba akulankhula ngati ndani?

“Kodi ndi ndani amene akufuna umboni? Nanga malamulo amawadziwa?

“Umboni ulipo n’chifukwa chake tikufuna kufufuza modekha kuti zomwe tipeze tipereke kwa adindo ena?

“Ngati akufuna umboni atilore tipange kafukufuku wathu kuti tiwapatse umboni wokwanira,” iwo adatero.

A Suleman atsutsa zomwe a Namalomba adalankhula, zoti Nyumba ya Malamulo ilibe mphamvu yochita kafufufuku.

“Ndiye umbuliwo, kaamba koti padakali pano akufufuza za kubedwa kwa mankhwala. N’chifukwa chiyani sakutiletsa?

“Tikufufuzanso za ngozi ya a Chilima. N’chifukwa chiyani sakutiletsa?” Takhalanso tikufufuza za nkhani ya chimanga, komanso za feteleza wotsika mtengo wa boma,” adatero a Suleman.

Iwo adati a Namalomba sakudziwa malamulo a dziko lino.

A Dustain Mwaungulu, omwe adapuma pa ntchito yoweruza milandu m’dziko muno, akugwirizana ndi a Suleman kuti Nyumba ya Malamulo ili ndi mphamvu yofufuza, koma osati yozenga ndi kugamula milandu.

A Suleman sakuonana ndi diso labwino ndi akuluakulu ena a boma kaamba koti akufuna kufufuza ziphuphu m’boma.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button