Nkhani

A Kaliati akadali m’manja mwa apolisi

Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM mayi Patricia Kaliati akhoza kukhala m’chitokosi ku mapeto kwa sabata ino m’chitokosi kuchokera pomwe apolisi adamumanga Lachinayi.

A Kaliati adamanga a Kaliati Lachinayi n’kuwatengera ku polisi ya Lingadzi. Kenako adawasamutsira ku likulu ya apolisi ku Area 30 mu mzinda wa Lilongwe ndipo dzulo masana adawasamutsira ku polisi ya Area 3 koma sanawatengere ku khoti komwe akadapeza mwayi wa belo.

Ali m’chitokosi: A Kaliati

Ndipo dzulo, akuluakulu a UTM dzulo adati kumangidwa kwa a Kaliati ndi ulenje wa boma wofuna kukhazika pansi onse omwe akupereka chiopsezo Ku bomalo.

Apolisi adamanga a Kaliati Lachitatu powaganizira kuti adagwirizana ndi anthu ena awiri kuti apalamule mlandu omwe apolisiwo sakuulula koma akuti ndi mlandu waukulu kwambiri ndipo ati ali ndi umboni waukulu.

Polankhula ndi atolankhani dzulo, mneneri wa chipanicho a Felix Njawala adati chipani cha UTM chimadziwa kale kuti a Kaliati amasakidwa ndipo adali pa mndandanda wa akuluakulu a ndale omwe boma likufuna kumanga.

“Zoti a Kaliati amasakidwa t ikuzidziwa ndipo apapa boma langopherezera zomwe timayembekezera. Koma ngati chipani sitikunjenjemera ndi zomwe akuchita chifukwa ndife madolo,” adatero a Njawala.

Akuluakulu a zipani zosiyanasiyana monga UDF, DPP ndi Aford adapita ku polisi kukaona a Kaliati.

Dzulo lomwelo, chipani cha UTM chidali ndi msonkhano wa komiti yaikulu yomwe amayenera kutsogolera a Michael Usi omwe ndi mtsogoleri wachipanicho koma sadapiteko.

A Njawala adatsimikizira Tamvani kuti msonkhanowo u d a t h e k a n d i p o adatsogolera ndi wachiwiri kwa mlembi wachipani koma adakana kuulula zomwe zidakambidwa ku msonkhanowo.

Nkhani ya y i kulu yomwe imayembekezeka k u k a m b i d w a k u msonkhanoko ndi yokhudza tsiku la konvenshoni komanso ndalama zomwe ofuna maudindo akuyenera kupereka kuti aimire maudindowo.

Mmbuyomu a Kaliati adalengeza kuti onse ofuna mpando wa mtsogoleri wa chipanicho ayenera kulipira K20 miliyoni koma a Usi amati ndalamayo yakwera kwambiri.

Kadaulo pa ndale a Wonderful Mkhutche adati ndalama zomwe chipani cha UTM chakhazikitsa kuti ofuna maudindo azipereka n’chiletso cha pansipansi kwa anthu ena.

“Ndalamazo zachuluka moti ena ngati amafuna maudindo sakwanitsa k u p e r e k a . A p a p a demokalase siyiyenda bwino,” a d a t e r o a Mkhutche.

Anthu 6 asonyeza chidwi chodzapikisana nawo pa mpandowu. Awa ndi a Usi, mayi Kaliati, a Matthews Mtumbuka, a Newton Kambala, a Dalitso kabambe ndi a Penjani Kalua omwe amatchuka kuti Fredokiss.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button