A ku Mozambique akulembetsa mavoti
Nzika zina za m’dziko la Mozambique zikulembetsa nawo m’kaundula wa mavoti ku Dedza popofuna kuti zidzavote nawo pa chisankho cha magawo atatu chomwe chilipo pa 20 May, 2014.
Mneneri wa polisi ku Dedza Edward Kabango wati panopa apolisi anjatapo kale nzika imodzi ya dzikokolo, Edward Tenganibwino, wa zaka 28, wochokera m’mudzi mwa Golong’ozo yemwe amafuna kulembetsa m’kaundulayu mwachinyengo.
Kabango wati Tenganibwino adanamiza akalaliki ochita kalemberayu kuti ndi Mmalawi ndipo amachokera m’mudzi mwa Katsekaminga ku Dedzako koma akalalikiwo adamuzindikira msanga ndi kumuneneza kupolisi.
Bungwe logwira ntchito zophunzitsa anthu la National Initiative for Civic Education (Nice) lati nzika zambiri za ku Mozambique zalowa m’dziko muno kufuna kudzalembetsa nawo koma zina zidabwezedwa akalaliki a kalemberayu atazitulukira.
Mkulu woyendetsa za maphunziro kubungweli, Patrick Siwinda, wauza Tamvani kuti asanu agwidwapo kale koma ena akadali zungulizunguli m’bomalo kuyesayesa kuti alembetse m’kaundulayu.
Iye wati ambiri mwa anthuwa akuti amafuna ziphaso zoponyera voti ndi cholinga choti azidzatha kutenga ngongole zotukulira ulimi wa kachewere kumabanki a m’dziko muno.
Siwinda wati ambiri mwa anthu achinyengowa akumagwiritsa ntchito ziphaso zolowera ndi kutuluka m’dziko za Malawi komanso ziphaso zoponyera voti za m’ndondomeko ya chisankho cha chaka cha 2009 ngati umboni kuti awalembe.
“Pa 2 November, bambo wina wa ku Mozambique adabwera ndi chiphaso cha ku Malawi kuti alembetse koma adabwezedwa,” adatero Siwinda.
Iye adati nthumwi za bungweli zati mchitidwewu ukuoneka m’malo olembetserako 13 a m’dera la Bembeke.
Siwinda wati madera omwe akukhudzidwa ndi mchitidwewu ndi Katsekaminga CDSS, Mazanjala, sukulu zapulayimale za Kapesi ndi Magaleta, sukulu zasekondale za Umbwi, Msambiro, Dedza Muslim Jamat, sukulu ya asungwana Achisilamu ya Dedza, Dedza CCAP, Dedza LEA, Dedza Community Hall ndi mudzi wa Dauya.
Bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission
(MEC) lati mchitidwe wolembetsa kapena kuthandizira munthu yemwe sali woyenera kulembetsa kuti alembetse ndi mlandu waukulu ndipo wolakwa akhoza kunjatidwa.
Wofalitsa nkhani m’bungweli Sangwani Mwafulira wati pofuna kuchepetsa mchitidwewu, zipani ndi mabungwe azisankha oyang’anira ndondomeko ya chisankho (monitors) kuchokera m’dera lomwe kukuchitikira ntchitoyi kuti azitha kuzindikira anthu ofuna kuchita zachinyengo.
“Ndi bwino kusankha nthumwi za m’dera lomwe kukugwiridwira ntchitoyi chifukwa sizivuta kuzindikira anthu. Komanso anthu akuyenera kuzindikira kuti kuperekera umboni wabodza kuti munthu ndi Mmalawi pomwe si Mmalawi woyenera kulembetsa m’kaundula ndi mlandu waukulu woti munthu akhoza kulipira ndalama zokwana K500, 000 kapena kukakhala kundende zaka ziwiri,” watero Mwafulirwa.