Nkhani

A Tembo asiya Amalawi m’misozi

Listen to this article

 Imfa ya mphangala ya ndale a John Zenus Ungapake Tembo yaonetsa kuti Amalawi ndi amodzi ngakhale kusiyana kwa zipani za ndale kumabweretsa kusemphana apo ndi apo.

Zotchulana maina onyogodola, kuima pa nsanja nkumanyozana kapena kuthothola nantheng a mmasamba a mchezo pa intaneti kudati ziii kuyambira Lachitatu pomwe a Tembo adatsamira mkono.

Adatisiya Lachitatu: A Tembo

Pafupifupi zipani zonse za ndale m’dziko muno zidatulutsa kalata zawo za likhuzo ndipo zonse msozi udali umodzi: “Tataya munthu wofunikira kwambiri, munthu yemwe adali chikhomo chathu.”

Naye mwana wa malemu a Tembo ,John Tembo Junior sadameze mtima polengeza nkhani yokhetsa msoziyo kwa atolankhani ku chipatala chomwe bambo ake adanyamukira ulendo wina.

“Tinkadziwa kuti izizi zidzachitika tsiku lina koma sitinkayembekezera kuti tsiku lake n’kukhala lero. Akubanja onse ngokhudzidwa ndi imfa imeneyi koma poti zachitika,” adatero John Tembo Junior.

Kudali pikitipikiti w a atsogoleri a zipani za ndale kukhamukira ku chipatalako kukatsimikiza za uthenga wodzidzimutsawo ndipo onse amavala nkhope za chisoni kusonyeza kukhudzika.

Mauthenga okhuza adali mbweee ndipo akunkira kuponyedwapa Intaneti, m’mawailesi, m’makanema ndi m’nyuzipepala kuchokera kwa andale ndi nthambi zina.

A Temb o omwe adamwal ira ndi zaka 91 adayamba ndale m’chaka cha 1960 pomwe adakhala phungu wa Nyumba ya Malamulo ali ndi zaka 27 ndipo dziko la Malawi litalandira ufulu wodzilamulira mu 1964, a Tembo adali mmodzi mwa anthu omwe mtsogoleri woyamba wa dziko lino a Hastings Kamuzu Banda ankadalira.

Mu mbiri yawo, iwo adakhala nduna yoyamba ya za chuma komanso adakhala m’mipando yaunduna yosiyanasiyana pa moyo wawo wandale.

Kuonjezera apo, a Tembo adakhalako mkulu wa banki yaikulu ya Reserve Bank of Malawi ndipo pa ulamuliro wa chipani chimodzi cha Malawi Congress Party, a Tembo adali mmodzi mwa akuluakulu odalirika.

N d a l e z i t a s i n t h a n’kubwera ulamuliro wa zipani zambiri, a Tembo adagwiritsitsa chipani cha MCP ndipo mpaka lero Amalawi akuwalira ngati mkulu wa mbali yotsutsa boma wolimba kwambiri.

Iwo adaimilira chipani cha MCP pa mpando wa Pulezidenti mu 2004 ndi 2009 koma ulendo onse uwiri adagonja kwa a Bingu Wa Mutharika poyamba pa tiketi ya United Democratic Front (UDF) kenako Democratic Progressive Party (DPP).

M u k h u z o l a ke , sipikala wa Nyumba ya Malamulo a Catherine Gotani Hara apereka sawatcha ya ulemu kwa a Tembo ngati mtsitsi ozama pa ndale komanso mtsogoleri wa mphamvu wa mbali yotsutsa boma.

N d i p o p o m w e t i m a s i n d i k i z a Tamvani L a c h i n a y i n’kuti ndondomeko ya mwambo woika m’manda thupi la a Tembo isanatulutsidwe.

Related Articles

Back to top button
Translate »