Nkhani

 Ma rodibuloku abwerere

Kadaulo pa za chitetezo a Loti Dzonzi omwe adakhalako mkulu wa apolisi ( I G ) m’dziko muno waunikira kuti kubwezeretsa zipata za m’misewu kungakhwimitse chitetezo.

Izi zikudza pomwe Amalawi akudzudzula apolisi kuti chitetezo chatsika m’dziko muno potsatira malipoti omwe akhala akumveka a anthu ophedwa mwankhanza, kuthyoledwa kwa magalimoto komanso umbanda wa ana anamasikini.

Sabata yathayi, anthu atatu odziwika adapezeka ataphedwa nkuponyedwa mmagalimoto awo komanso ophunzira kunsukulu ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) adaphedwa n’kuponyedwa m’chitsime ku Dowa.

Povomer eza nkhan izo, mneneri wapolisi a Peter Kalaya adati ziwembu zonsezo zimaoneka kuti zidali zokonzekera bwinobwino chifukwa cholinga cha achiwembuwo chikuoneka kuti kudali kupha.

“Tikaunika momwe z i w e m b u z o n s e z o zidakhalira, tikuona kuti achiwembuwo cholinga chawo chidal i kupha ndipo tikufufuza kuti tigwire omwe adachita chiwembucho,” adatero a Kalaya.

Koma a Dzonzi adati kupezeka kwa zipata z a p o l i s i m m i s e w u kumapeleka mantha kwa anthu omwe akufuna kupanga chiwembu chifukwa mpata ndi malo opangira chiwembu amasowa.

“Apolisi akuyenera kuwonjezera kupezeka kwawo mmizinda ndi mmisewu. Zipata zapolisi zija nzofunika kwambiri chifukwa zimathandiza k u p e w a z i w e m b u chifukwa anthu amawopa kuti akhoza kukumana ndi apolisi nthawi iliyonse,” adatero a Dzonzi.

Mabungwe omwe si aboma, zipani zotsutsa boma komanso aMalawi akhala akupempha boma kuti likwimitse chitetezo m’malo osiyanasiyana.

Izi zidayamba pomwe anthu adayamba kugawana makanema a anthu othyola magalimoto, anthu ovulazidwa ndi ana a masikini komanso za anthu omwe aphedwa posachedwapa.

Koma nduna ya za chitetezo cha m’dziko a Ken Zikhale Ng’oma adati Amalawi asade nkhawa chifukwa chitetezo chikadali bwinobwino.

Iwo adati mantha achuluka chifukwa nkhani zokhudza kuphedwa kwa a Allan Wittika womwe ankagwira ntchito ku kampani ya Cocacola, a Agness Katengeza omwe ankagwira ntchito ku Reserve Bank of Malawi komanso bambo yemwe adapezeka ataphedwa ku Area 25 ku Lilongwe.

Mphunzitsi wa za chitetezo ku Mzuzu University a Aubrey Kabisala adati kutsika kwa chitetezo kwayenera kukhala ndi gwero lake lomwe boma likuyenera kufufuza bwino.

“Chilipo chomwe c h a c h i t i t s a , sizingangobwera ayi koma sitepe yoyamba nku f u f u z a chomwe chatsitsa dzaye kuti zinthu zifukwa pamenepa kenako n’kupeza njira zokonzera vutolo,” ada t e r o a Kabisala.

Nayo komiti yoona zachitetezo ku Nyumba ya Malamulo yayitanitsa mkulu wapolisi ndi nthambi zina zachitetezo kuti akalongosole bwino zokhudza chitetezo cha m’dziko.

Wapampando wa komitiyo a Ralph Jooma adati komiti yawo ili n d i c h i y e m b e ke z o chot i akuluakuluwo akalongisola momwe zinthu zilili kuti mitima ya Amalawi ikhazikike.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button