Achikulire asowa thandizo madzi atavuta

Limodzi mwa mabungwe omenyera ufulu wa anthu achikulire m’dziko muno lati ena mwa achikulire amene adakhudzidwa ndi madzi osefukira sabata ziwiri zapitazo sakulandira thandizo loyenera kuchokera ku boma.

Madzi osefukirawa akhudza maboma 15 mwa 28 m’dziko muno, ndipo anthu 868 895 ndiwo akusowa pokhala chifukwa cha vutoli.

Mwa anthuwa, 672 ndiwo adavulala pomwe 56 adaphedwa, malinga ndi kalata yomwe bungwe la Unicef idatulutsa Lachitatu.

Kazembe adagonekedwa kuchipatala

Pakadalipano anthu 90 000  akukhala m’misasa yomwe yakhazikitsidwa m’maboma ena monga Chikwawa ndi Nsanje.

Komatu anthuwa akulandira thandizo loperewera lomwenso likumafika mochedwa malinga ndi kalata yochokera ku bungwe la European Commission’s Joint Research Centre(JRC).

Koma mwa anthuwa achikulire ndiwo akuvutika kwambiri chifukwa akungodalira thandizolo chifukwa cha ukalamba.

Bungwe la Friends for the Elderly lati kafukufuku wake akuonetsa kuti anthu achikulire ena sadalandirebe thandizo mpaka lero ngakhale ngozi ya madzi osefukirawa idagwa sabata zitatu zapitazo kuchokera pa 5 March.

Malinga ndi kalata yomwe bungwelo latulutsa yosainidwa ndi mmodzi mwa oyendetsa bungwelo Mike Magelegele, bungwe lake lidapeza kuti vutoli lakhudza achikulire omwe amakhala okha opanda owasamalira komanso m’malo ena kufikamo.

Bungwelo lati mmodzi mwa nkhalambazi, Gogo Naphiri yemwe amakhala m’mudzi mwa Namboya kwa T/A Machinjiri m’boma la Blantyre adamupeza ali yekhayekha opanda thandizo ndipo kuti anthu a m’mudzi mwake sangamuthandize chifukwa ati ndi mfiti.

Naye gogo Fanny Kazembe wa zakat 56 yemwe ndi Nyakwawa N’nunkha ya kwa T/A Mpama m’boma la Chiradzulu yemwe nyumba yake idamugwera pa March 7 ndipo adavulala phazi, kumsana ndi m’mapewa mpaka kugonekedwa pachipatala cha Nguludi thandizo lochokera kuboma monga chakudya ndi zina silinamupeze.

Nthambi ya boma yowona za ngati zogwa mwa dzidzidzi silidatiyankhe mafunso omwe tidalitumizira okhudza nkhaniyi lomwe Tamvani udafuna kumva dongosolo la boma pa chisamaliro chopita kwa nkhalamba. n

Share This Post