Nkhani

Agulitsa mwana ndi K18 miliyoni

Nkhondo ndi anansi. Wodya naye mbale imodzi ndiye amakupereka kwa adani. Izi zapherezera kwa mwana wina wa zaka 11 yemwe msuweni wake anamutsatsa pa mtengo wa K18 miliyoni.

A Madalitso Wyson, yemwe ali ndi zaka 22, adapita kusukulu kwa mwanayu ku Chingazi, m’dera la Ntambanyama m’boma la Thyolo pa nthawi yopuma ndi kumutenga mwanayo. Apolisi m’boma la Thyolo atsimikiza za nkhaniyi.

Malinga ndi mneneri wa polisi m’bomalo a Amos Tione, a Wyson atamutenga mwanayo yemwe ali m’sitandade 2, adapita naye kwa chibwenzi chake komwe anakagona kwa tsiku limodzi.

“Zonsezi zimachitika makolo a mwanayo asakudziwa kanthu,” anatero Tione.

Iwo adati kutacha m’mawa, Wyson adamutenga mwanayo kupita naye pamsika wa Ntambanyama pomwe anakakumana ndi sing’anga wina ndi kumutsatsa malondawo.

“Koma sing’angayo anatsina khutu anthu ena komanso apolisi ndipo a Wyson adatsekeredwa pamlandu wozembetsa ana mosemphana ndi gawo 15 la malamulo wozembetsa anthu,” adatero a Tione.

Msangulutso udacheza ndi sing’anga Billy yemwe anati zokambirana zake ndi Wyson zidaonetsa kuti munthu yemwe mnyamatayo anapangana naye kugula mwanayo anamugwiritsa fuwa lamoto.

Billy adati Wyson atafika pamalo ake a ntchito anamuitanira pambali n’kumuuza kuti pali bizinesi ya mwanayo.

“Adandiuza kuti adapangakonso bizinesiyi mmbuyomo ndi anzake omwe adamupusitsa ndi kuthawa ndi ndalama, ndipo ulendo uno adaganiza zochita bizinesiyo yekha,” adatero a Billy.

Iwo adati Wyson adawauzanso kuti ngati akufuna akhoza kumupatsa wokonzakonza.

“Pofuna kupulumutsa moyo wa mwanayo, ndidamuyenda pansi ndi kupeza mkulu wina yemwe adanamizira ngati wogula kwinaku ndikuimbira foni apolisi omwe adadzamumanga,” adatero a Billy.

Iwo adati aka si koyamba chifukwa mmbuyomu adafikiridwakonso ndi anthu ena omwe adawauza kuti akufuna chizude pa mtengo wa K10 miliyoni ndipo adazindikira kuti iyi inali njira yongozembaitsa chifukwa anthuwo amafuna munthu.

Ndipo mkulu woyang’anira maphunziro m’boma la Thyolo a Godfrey Kubwense adatsimikiza kuti mphunzitsi wamkulu wa pasukulu ya Chingazi adawadziwitsa za nkhani ya mwanayo.

Nkhani zozembetsa anthu zakhala zikukula m’dziko muno. M’chaka cha 2020 anthu 688 adapulumutsidwa ku mchitidwewu.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button