Nkhani

Agwira othandiza akunja kupeza zitupa zaunzika

Listen to this article

Mmiyezi iwiri yokha chiyambireni kalembera wa zitupa za unzika, Amalawi ena ayamba kugwidwa akuthandiza nzika za mayiko ena kupeza zitupazi.

Akuluakulu ena ati uku n’kusowa chikondi ndi dziko lawo la Malawi.

Ntchito ya kalembera ili mkati m’chigawo cha pakati

Nzika zitatu za ku Mozambique zagwidwa kale m’boma la Dedza pomwe zimafuna kulembetsa m’kaundulayu pamalo olembetsera a Umbwi mothandizidwa ndi mayi wa Chimalawi.

Mneneri wapolisi ku Dedza Edward Kabango adati nzika za ku Mozambique ndi Samalani Joseph wa zaka 21, Patrick Machaka wa zaka 32, Chewami Ali wa zaka 25 ndipo onse ndi ochokera ku Angonia, m’chigawo cha Tete ku Mozambique pomwe m’zimayiyo ndi Angellina Lameck wa zaka 36 wochokera m’mudzi mwa kapalamula ku Dedza. Iwo akaonekera kukhoti posachedwa.

Mneneri wa nthambi yoyendetsa kalemberayu ya National Registration Bureau (NRB) Norman Fulatira watsimikiza kuti mzimayi wa ku Malawi wamangidwa limodzi ndi nzika za ku Mozambique pomuganizira kuti amafuna kuzithandiza kupeza zitupa za unzika.

Iye adati mayiyo akumuganizira mlandu wofuna kuthandiza nzika za dziko lino kupeza zitupa zaunzika popereka umboni wabodza, motsutsana ndi malamulo a pulogalamuyi.

“Boma likufuna kuthandiza Amalawi popangitsa zitupazi chifukwa nzika za maiko ena zakhala zikuwadyera masuku pamutu ndiye Amalawi omwewo akuthandizanso alendowo kupanga chinyengo, kumeneku n’kusowa umunthu,” watero Fulatira.

Iye wati kuthandiza nzika za mayiko ena kulembetsa mwachinyengo ndi mlandu pa malamulo a nthambiyo ndipo munthu akhoza kukasewenza zaka 5 ndi kupereka chindapusa cha K1 miliyoni akapezeka wolakwa.

Kabango wati awiri mwa anthuwo adapezeka ndi zitupa za unzika za m’dziko la Mozambique ndipo adavomera kuti amafunadi kupeza zitupa za unzika wa Malawi.

“Titawafusa bwinobwino adaulula kuti cholinga chawo chidali choti azitha kulandira thandizo la zaumoyo m’zipatala za ku Malawi mosavuta. Akuti kwa iwo, thandizo la msanga la za umoyo amalipeza ku Malawi,” adatero Kabango.

Iye adati anthuwa akuimbidwa mlandu wopereka umboni wabodza kwa akuluakulu a kalembera zomwe zikutsutsana ndi gawo 43 la malamulo oyendetsera ntchito za NRB.

Pochita kalemberayu, nthambiyo ikufuna umboni ochokera kwa mafumu kapena zitupa zina monga zoyendera, zoyendetsera galimoto, zakubadwa kapena ukwati, zomwe zikusonyeza kuti munthu ndi Mmalawi.

Apa zikutanthauza kuti wofuna kuthandiza alendo kupeza zitupa za unzika, awathandize kupeza umboni onsewu, zomwe zikutanthauzanso kuti mkatikati mwa dongosololo mwadutsa katangale omwe ndi mlandu wina pa malamulo a dziko lino.

Mneneri wapolisi, James Kadadzera, wati mchitidwewu ndi wobwezeretsa zinthu mmbuyo chifukwa njira ya zitupayi ndi imodzi mwa njira zomwe boma likufuna kuti lizidziwira nzika zake kupangira pa mavuto komanso kowopetsa nzika za mayiko ena kupanga zaupandu mmawanga Amalawi.

“Zitupazi zikulowa pambiri chifukwa kuchitetezo nako  zikukhudzako. Mmbuyomu tidali ndi vuto loti nzika za mmaiko ena zimatha kupanga chiwembu n’kumaoneka ngati Amalawi ndiye zimayipitsa mbiri yathu.

“Ntchito ya zitupayi ikayenda bwinobwino ndiye kuti mavuto onsewa adzatha chifukwa tizidziwana kuti uyu ndi Mmalawi kapena ongobwera kotero chitetezo chikhwima komanso mbiri yathu siyionongeka,” watero kadadzera.

Nduna ya za m’dziko ndi chitetezo Grace Obama Chiumia wati Amalawi akuyenera kukhala ndi mtima wokonda dziko lawo pothandiza boma kukwaniritsa ndondomeko zomwe cholinga chake n’kuwatumikira mwaukadaulo.

“Pologalamu ya zitupa si ya munthu kapena mtundu ayi koma ya Amalawi ndiye tikuyenera kugwirana manja tonse n’kuthandizana ndi boma kuti pologalamuyi iyende bwino chifukwa patsogolo ndife tomwe tidzaimve kukoma,” watero iye.

Related Articles

Back to top button