Akangalika ndi ulimi wa mthirira

Mlimi wochenjera monga NELLIE NYONI wa m’boma la Balaka amayambiratu ulimi wa m’chilimwe mvula ikamapita kumapeto kuti asavutike kwambiri ndikuthirira. Tikunena pano adabzala kale chimanga komanso nyemba  ndipo posachedwapa ziyamba kubereka. ESMIE KOMWA adacheza ndi mlimiyu motere:

Ulimi wa m’chilimwe umaposa wa m’dzinja

Kodi n’chifukwa chiyani mumafulumira kuyambapo ulimi wa mthirira?

Choyambirira ndimafuna kuti ndigwiritse ntchito chinyezi chochuluka chomwe chimapezeka mvula ikangosiya kugwa kuti mbewu zikamadzafuna madzi owonjezera ndidzangothirira kanthawi kochepa basi zatheka. Chifukwa china n’choti ndimafuna ndizipezeka ndi mbewuzi pafupipafupi kuti ndizipeza phindu lochuluka.

Nanga mudayamba liti ulimi wa mthirira?

Ulimiwu ndidayamba mu 2004.

Kodi chidakukopani pa ulimiwu n’chiyani?

Ndidaona kuti mbewu za mthirira zimagulitsidwa pa mtengo kusiyana ndi zodalira mvula ndipo ichi n’chifukwa chomwe ndimazilimbikira.

Nanga mumalima mbewu zanji?

Ndimalima mbewu zosiyanasiyana monga tomato ndi kabichi koma kwambiri ndimaonjeza chimanga.

Kodi mumalima mbewuzi pamalo okula bwanji?

Malo womwe ndimachitirapo mthirirawu ndi wokwana ma ekala 6 ndi theka.

Nanga zikayenda bwino mumapeza ndalama zochuluka bwanji pakamozi?

Mbewu yomwe ndimaiwerengetsera bwino ndi ya chimanga chifukwa ndimailima mochuluka monga ndanena kale. Chimangachi chikakhwima ndikugulitsa chachiwitsi ndimatha kupeza K600 000 ndipo zikavutirapo K500 000.

Kodi chinsinsi chanu chagona pati?

Chinsinsi changa ndikusamalira mbewu  kuti zichite bwino. Ndimaonetsetsa kuti zizipeza madzi wokwanira, ndimathira feteleza, ndimapalira komanso kuthana ndi zilombo zoononga kuti zichite bwino. Ubwino wa mbewu za mthirira ndiwoti zikangotheka ndimadziwiratu kuti zanga zayera.

Kodi mumagwiritsa ntchito mthirira wanji?

Kwa zaka zonsezi ndakhala ndikugwiritsa ntchito ma water cane kuthiririra mbewu zanga koma padakali pano ndagula pampu yopopera madzi yogwiritsa ntchito petulo.

Nanga ndi mavuto anji omwe mumakumana nawo pogwiritsa ntchito mthirira woterewu?

Kunena zoona mthirira wa mtunduwu ndiwopweka kwambiri. Tangoganizani kuti munthu ukwanitse kuthirira malo wokula motere sizamasewera koma khama langa pa ulimiwu ndilomwe limandichititsa kuti ndizilimbikirabe.

Nanga ndi mavuto anji omwe mumakumana nawo pa ulimiwu?

Vuto lalikulu ndikusowa kwa zipangizo za mthirira za makono zogwiritsa ntchito madzi ochepa. Vuto lina ndikusowa kwa madzi othiririra mbewu makamaka tikamayandikira nyengo yotentha  zitsime zomwe timadalira nthawi zina zimaphwa ngati mvula siidagwe yokwanira. Izi zimachititsa kuti tidukize panjira n’kumadikirira mvula m’malo moti tizilumikiza kwa chaka chonse. Chinthu chokhumudwitsa kwambiri n’choti ulimiwu timangozichitira popanda alangizi a mthirira ndipo ndimadabwa ngati alipo m’dziko muno.

Nanga masomphenya anu pa ulimiwu ndiwotani?

Ndikufuna mtsogolomu nditaika mthirira wa makono uja amalumikiza mapaipi ndikumangotsegula madzi kuti azifikira mbewu okha. Mthirira woterewu umafuna mlimi akhale ndi matanki, zitsime zakuya ndi zopopera madzi zogwiritsa ntchito zipangizo zoyendera magetsi kapena mphamvu ya dzuwa. Izi zidzandithandizira kuti ndizitha kukhala ndi madzi kwa chaka chonse komanso kupopa  mosavuta ndikumathiririra mbewu zanga.

Kodi mudzapitiriza kulima mbewu zomwe mukulima panopazi?

Ayi ndikufuna ndidzayambe ulimi wa kachewere chifukwa ndidamva kuti ndiwaphindu kwambiri koma ndimakanika kuyamba panopa chifukwa cha mavuto omwe ndanena aja. Kabitchi ndi mbewu ina yomwe ndimaganiza kuti ndidzaikirapo mtima.

Nanga muchita chiyani kuti mukwaniritse masomphenyawa?

Pa ine ndekha ndikuona kuti ndizovutirapo chifukwa zipangizo za mthirira wa mtunduwu ndizokwera ntengo kwambiri. Ndidakakonda padakapezeka mabungwe omwe akhoza kundithandiza kufikira masomphenyawa. Tidayetsera kuwafotokozera a ku nthambi yoona za ulimi wa mthirira koma adangotiyankha kuti tikuthandizani kutenga ngongole ku banki. Ngakhale adatilonjeza motere koma tikuona kuti izi sizingachitike choncho ndikupempha akufuna kwabwino kuti andithandize.

Share This Post