Gwiritsani bwino ntchito chinyezi kuti mupindule

Potsatira mvula yochuluka yomwe yagwa m’chakachi, akatswiri a za kafukufuku wa ulimi wa mthirira  akuti alimi a m’zigwa za dziko lino, m’mbali mwa mitsinje komanso omwe ali ndi madambo agwiritse ntchito chinyezi kulima mbewu zosiyanasiyana ndipo aphula kanthu.

M’modzi mwa akatswiriwa, Isaac Fandika wa ku Kasinthula Research Station m’boma la Chikhwawa adati madera monga a m’chigwa cha mtsinje wa Shire komanso oyandikira mitsinje ndi madambo  madzi amakhala pafupi.

Maenje obzalamo mbewu akhale akuya

Iye adafotokoza kuti chofunikira ndikuonetsetsa kuti maenje obzalamo mbewu azikhala akuya mosachepera masentimita 30.

“Izi zimathandiza mbewu kufikira madzi mu nthaka  mosavuta  choncho zimachita bwino kwambiri,” iye adatero.

Chachiwiri, iye adati alimi atsatire njira zothandiza kusunga chinyezi kwa nthawi yaitali monga kuvindikira dothi ndi mapesi, udzu, masamba a mitengo kapena kuchita kasakaniza ndi mbewu zoyanga kuti madzi asathawe msanga mu nthaka.

Zotsatira zake, Fandika adati malo okhala madziwa sapita pansi kwambiri kotero mbewu zimawagwiritsa ntchito  kwa  nthawi yaitali.

Katswiriyu adati m’madera momwe chinyezichi chimakhala chokwanira kwa nthawi yotalikirapo alimi akhoza kulima mbewu monga chimanga.

“Mbewu zocha msanga monga nyemba kapena zopirira ku ng’amba ndi za mizu yaitali zimachita bwino mosavuta ndi chinyezichi,” iye adatero.

Katswiri wa mbewu za mtundu wa mbatata ku Bvumbwe Research Station Miswell Chitete adati mbatata ikhoza kuchita bwino m’madera ambiri momwe muli chinyezi kusiyana ndi chinangwa.

Malingana ndi Chitete, ngakhale chinangwa ndichopirira ku ng’amba chimatenga miyezi 12 kuti chikhwime choncho kubzala panopa ndikuchedwa kwambiri pamene mbatata m’miyezi inayi yokha imakhala yatheka.

“Kubzala chinangwa padakali pano  chidzangokhala ka nthawi kochepa pa chinyezi ndikulowa m’chilimwe koma mbatata pomadzafika nthawiyi idzakhala itacha,” iye adatero.

Iye adaonjeza kuti kwa mlimi yemwe amachita mthirira, akhoza kulima chinangwa panopa ndikudzathirira nthawi yochepa.

Mkulu wa nthambi ya za kafukufuku wa mbewu  ya Lifuwu ku Salima Cornwell Iman adati  alimi omwe amachita ulimi wa dzinja ino ndi nthawi yabwino yoti ayambepo kubzala mbewu.

Iman adati ulimi wa dzinja sutanthauza kuthirira kokha komanso kugwiritsa ntchito chinyezi pobzala mbewu zosiyanasiyana.

“Ulimi wa mtunduwu ndiwosavuta komanso wopindulitsa chifukwa mlimi sataya mphamvu, nthawi ndi ndalama zothiririra mbewu chifukwa zimangodzikulira zokha pa chinyezi paja,” iye adatero.

Mkuluyu adafotokoza kuti alimi akhoza kugwiritsa ntchito chinyezichi kulima mbewu za masamba zomwe sizichedwa kucha ndikumapindula nazo.

M’modzi mwa alimi omwe amagwiritsa ntchito chinyezi polima mbewu za masamba ndi Elison Banda wa m’boma la Lilongwe  ndipo akuti momwe mvula yagwera m’chakachi ali ndi chikhulupiriro choti mbewu zicha mosalira mthirira.

“Ndimalima mbewu zosiyanasiyana ku dimba mvula ikangoleka koma malingana ndi magwedwe a mvula m’zaka za m’mbuyomu, ndimachita kuzimalizitsa ndi mthirira.

“Kale mvula ikugwa yokwanira zimenezi sizimachitika choncho momwe yagwera m’chakachi ndikuyembekezera kuti zicha osathirira,” iye adatero.  

Share This Post