Nkhani

Akufuna boma lichitepo kanthu pa za zigandanga

Akadaulo oimira magulu osiyanasiyana ati boma likuyenera kuchitapo kanthu pa za zigandanga za zikwanje zomwe zakhala zikusokoneza zionetsero osati kungolankhulapo basi.

Izi zikudza pomwe mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adadzudzula mchitidwewo ndi kulamula kuti nduna ziwiri, yoona za chitetezo cha m’dziko a Ezekiel Ching’oma komanso nduna ya asilikali a nkhondo a Monica Chang’anamuno kuti apereke malipoti.

“Ndikufuna kulandira malipoti pa zomwe zidachitika ndipo tidzagwiritsa ntchito malipotiwo kuti tidzaone momwe tidzapangire pa nkhani imeneyi,” adatero a Chakwera.

Koma wapampando wa mabungwe oona kuti chisankho chiziyenda mwa chilungamo a Benedicto Kondowe ati nkhani ya zikwanje si yofunika kuitenga mwa chibwana chifukwa ikhonza kudzabala mavuto mtsogolo.

Iwo ati pakufunika kupanga zoti anthu akhalenso ndi chikhulupiliro mwa apolisi ndi asilikali chifukwa nkhani ya chitetezo makamaka pomwe dziko likulowera ku Chisankho Chachikulu.

“Timayenera kuona zotsatira za zomwe a Chakwera adanena chifukwa ndi njira yokhayo yomwe Amalawi angakhale n’chikhulupiriro. Kungolankhula popanda chochitika kulibe tanthauzo. Chete ngati ameneyu akhoza kusokoneza zisankho zomwe tikuyembekezera,” adatero a Kondowe.

Iwo adati momwe zinthu zilili, mpofunika magulu osiyanasiyana monga mabungwe ndi nyumba zofalitsa nkhani atenge gawo lalikulu kufukula zinthu zobisika kuti chilungamo chizioneka.

Mneneri wa bungwe la akadaulo pa za ndale a Mabvuto Bamusi nawo adati kupanda kuchitapo kalikonse pa za azikwanjewo kukhoza kupereka chithunzithunzi choti anyamatawo ngotumidwa.

“Izizi n’zomwe zidakambidwa kale ku msonkhano wa PAC zoti apolisi akuyenera kumagwira ntchito yawo mosaona nkhope ndipo adalonjeza kuti pakachitika za mtopola ngati omwe udachitika pa zionetsero zapitazo azichita machawi ndi kafukufuku.

Wapampando wa Human Rights Consultative Committee a Robert Mkwezalamba adati ngakhale kuti n’zomveka kuti a Chakwera adadzudzula mchitidwewo, Amalawi akadakondwa anthu amtopolawo atafufuzidwa ndi kuyankha milandu yawo.

“Tili mu nthawi yoopsa kwambiri apapa chifukwa kuangolakwitsa pang’ono, anthu akhoza kumaona ngati n’zokonza, kafukufuku akuyenera kuchitika ndithu chifukwa zigandangazo zidachita zolakwika kwa anthu omwe adalibe zida,” adatero a Mkwezalamba.

Polongosolera anthu omwe adasonkhana ku msonkhano wa PAC, mkulu wapolisi a Merlyne Yoramu adatsimikiza kuti sadzasekelera anthu osokoneza zionetsero za bata komanso kuti omwe adachita za mtunduwo mmbuyomo akufufuzidwa.

Nkhani ya zipolowezo idautsa mapiri pa chigwa mpaka nthumwi zoyimirira maiko ena zidadzudzulapo kuti apolisi sadapange zolongosoka poonerera anthu ochita zionetsero sabata akuchitidwa nkhanza.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button