Nkhani

Kampeni iyamba lolemba

Chisankho cha 2025 chifika gawo lina Lolemba likudzali pomwe bungwe loyendetsa zisankho la MEC lidzakhazikitse misonkhano yokopa anthu.

Malingana ndi ndondomeko za kampeni zimene zili m’malamulo oyendetsera chisankho, ofuna kupikisana nawo sadzaloledwa kugwiritsa ntchito mawu kapena khalidwe lomwe lingayambitse mkangano ndi ziwawa.

A Kajoloweka: Ziwawa ayi. | Nation

Pa mbali pa izi, ndondomekoyo ikuletsa kunyozana potengera kuti wina ndi mwamuna kapena mkazi, ikupereka mphamvu kwa apolisi ndi asilikali kuteteza anthu komanso ikulimbikitsa mafumu kuti apewe kukondera ndi kulola aliyense wotsata ndondomeko kuchititsa msonkhano wokopa anthu popanda zopinga.

Malingana ndi mneneri wa bungwe la MEC a Sangwani Mwafulirwa, zipani komanso oima pa okha akhale ndi mfundo za chitukuko komanso zobweretsa umodzi ndi chiyembekezo.

“Anthu amafuna kumva zomwe adindo awakonzera osati kumenyana ndi kuopsezana. Mkangano kapena kuopsezana kumangotaitsa nthawi mmalo momatambasula masomphenya,” atero a Mwafulirwa.

Motsatira malamulo, kampeniyi ikatsegulidwa Lolemba idzatenga masiku 60 ndipo adzaitseka pa 14 September. Motsatiranso malamulo, apa ndiye kuti adzangokhala masiku awiri kuti Amalawi aponye voti kusankha mtsogoleri wa dziko aphungu a Nyumba ya Malamulo komanso makhansala.

Pofuna kuti zipani zidzatsatire malamulo a kampeni, bungwe la MEC lakhala likukumana ndi zipani za ndale komanso mabungwe okhudzidwa kukambirana za chisankho.

Kadaulo pa ndale a George Phiri adati kulumikizana moyenera pomwe chisankho chikuyenda kumachepetsa chikaiko komanso kumaunikira momwe andale angapangire mfundo zawo.

“N’zofunika kwambiri kulumikizana chifukwa pakangokhala chikaiko pa momwe zinthu zikuyendetsedwera, kampeni ikhoza kusanduka bwalo la ziwawa ndi mikangano ndiye zimenezi n’zosathandiza,” adatero a Phiri.

Mneneri wa apolisi a Peter Kalaya adati apolisi adakhazikitsa kale ndondomeko zolimbikitsa bata ndipo akuyembekezera kuti zipani za ndale zidzatsatira ndondomekoyo.

“Ndife okonzeka kale chifukwa ndondomeko idakhazikitsidwa kale ku Lilongwe, sitikufuna kudzawona ziwawa zilizonse. Chachikulu, atsogoleri adzakhale chitsanzo chabwino kwa achinyamata a m’zipani zawo,” adatero Kalaya.

Mkulu wa bungwe la achinyamata la Youth and Society (YAS) a Charles Kajoloweka adati achinyamata asadzalole kugwiritsidwa ntchito yochita ziwawa koma mmalo mwake azitenga gawo popanga nawo mfundo za chipani kuti zikhale zokomera achinyamatawo.

“Ino si nthawi yoti achinyamata azikhala kalikiliki kuchita ziwawa, tikuyenera kugwirana manja n’kumenya nkhondo yokomera ufulu ndi udindo wathu kuti tidzakhale atsogoleri odalirika,” adatero a Kajoloweka.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button