Akulipitsa kulembetsa khadi

Anthu ena amene sadalembetse nambala zawo akulirira kuutsi pamene ma agenti ena akuwauza kuti alipire ngati akufuna nambala yawo ilembetsedwe.

Izi zikudza pamene makampani a foni za m’manja a Airtel ndi TNM adachotsa nambala zimene sizidalembetse pofika pa 30 September chaka chino.

Kulembetsa makadi ndi kwa ulere

Ngakhale kampanizi zidachotsa nambala zina, eni nambalawo ali ndi mwayi wokalembetsa nthawi iliyonse mwaulere.

Koma izi zikusiyana ndi zimene anthu ena akukumananazo pamene akupemphedwa kulipira kuti nambala yawo ilembetsedwe.

M’boma la Mulanje ndi Thyolo anthu ena akulipira kuti alembetse nambala zawo.

Mtolankhaniyu atayendera malo ena ku Chirimba mafupi ndi sitolo ya Macsteel adauzidwa kuti alipire K300 kuti nambala yake ya Airtel ilembetsedwe.

“Tikuyenera tigule mayunitsi a K300 omwe timalowera mu system ya Airtel kuti nambala yanu ilembetsedwe. Koma nambala yanuyo idadulidwa mwezi wapitawo zomwe zimapangitsa kuti ntchito yathu ikhale yovuta,” adatero agentiyo.

Titamuuza kuti tili ndi K100, iye adakananso kuti ndalamayo yachepa chifuwa polingalira kukula kwa ntchito yolumikizira nambalayo.

Mneneri wa kampani ya Airtel Norah Chavula-Chirwa adati ndi wodzidzimuka kuti anthu ena apezerapo mwayi kumabera makasitomala awo pamene akulembetsa nambala zawo.

Iye adati kampani yawo iyesetsa kuyenda m’midzi kulangiza anthu kuti sakuyenera kulipira polembetsa nambala.

“Tikulangiza makasitomala athu kuti aimbe 121 ngati wina wawauza kuti alipire polembetsa nambala yawo. Ngatinso m’deralo kuli ofesi yathu, athamangireko kuwamuneneza agent amene akulipiritsayo.

“Apo ayi athamangire kupolisi kukanena. Pamene akuimba 121, ayenera adziwe code ya agent-yo kuti tichotse nambala yake,” adatero Chirwa.

Naye mneneri wa kampani ya TNM, Daniel Makata adati alandira nkhani zotere m’boma la Mulanje komwe agent akufuna ndalama kuti alembe nambala.

Makata adati kampani yawo idalemba ntchito ma agent oposa 2500 m’madera onse a dziko lino kuti alembe onse amene ali panetiweki ya TNM.

“Ifeyo tidawalemba ntchito, ndi kulakwa kuti nawonso ayambe kulipiritsa makasitomala athu.

“Anthu adziwe kuti kulembetsa nambala ndi kwaulerere, sakuyenera kulipira kanthu pa ntchito imeneyi. Ngati wina wakupemphani ndalama chonde tidziwitseni apo ayi pitani kupolisi,” adatero Makata.

Makata adati pofika pa 30 September, kampani yawo n’kuti italemba makasitomala 75 pa 100 alionse.

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.