Chichewa

Akupha makwacha ndi nkhumba

Listen to this article

Pamene alimi ena akugulitsa ziweto zawo kwa mavenda motsika mtengo, Chawezi Nyirenda yemwe ndi mlimi wa nkhumba ku Lilongwe akupha makwacha a nkhaninkhani popha khumba zake zikakula, kuzikonza mopatsa kaso n’kumagulitsa yekha. ESMIE KOMWA adacheza naye motere:

Kodi chidakuchititsani kuti muyambe kukonza nyama ya nkhumba zanu n’kumagulitsa nokha n’chiyani?

Nditakhala pansi n’kulingalira mozama ndidaona kuti mavenda, komanso m’makampani ogulitsa nyama  amatigula pa mtengo wotsika chonsecho ukapha wekha n’kugulitsa amapeza phindu lochuluka.

Ndalama zonsezo?

Inde chifukwa ine nkhani yoweta nkhumba ndidapita nayo patali ndipo ikakula anthu amadziwanso kuti ntchito yagwirika.

Kodi ulimi wa nkhumba mudayamba liti?

Ulimiwu ndidayamba mu 2012 ndili Folomu 4.

Nanga mudayamba ndi nkhumba zingati?

Ndidayamba ndikuweta nkhumba 4 za mtundu wa trister ndipo zazikazi zidalipo zitatu ndi yaimuna imodzi. Pamene timalowa mu 2013 zidali zitaswana n’kufika pa 42. Imodzi mwa nkhumba zazikazizo idakalipobe ndipo yakhala ikuswa kokwana ka 12.

Kodi chidakukopani mu ulimiwu n’chiyani?

Ndidaona kuti nkhumba sizichedwa kuswana komanso sizivuta kuweta choncho ndi ulimi woti munthu ukhoza kutukuka nawo mu nthawi yochepa utaikirapo mtima.

Nanga padakali pano muli ndi nkhumba zingati?

Zambiri ndagulitsa posachedwapa kuti ndikonzenso makola choncho zatsala 20 zokha, koma zimafika 150.

Nanga ndi zinthu ziti zomwe mungaloze kuti mudazipeza kuchokera mu ulimiwu?

Kuchokera mu nkhumba mwatuluka famu  dzina lake  Step by Step  yomwe ili m’mudzi mwa Chimpumbulu m’boma la Lilongwe. Pafamuyi pali ziweto monga, ng’ombe za mkaka, mbuzi, nkhosa, nkhuku zachikuda, nkhanga, abakha, mbira ndi mbewu zakudimba ndipo padakali pano ndakumbitsapo madamu ansomba. Zonsezi zachokera mu ulimi wa nkhumba womwewu. Kuonjezera apo, ndikulipirira ana sukulu komanso kusamalira banja langa mosavuta.

Kodi chinsinsi chanu chagona pati?

Chinsinsi changa ndikuzitsamalira bwino basi. Ndimazidyetsa katatu patsiku. Mwachitsanzo, chakudya cholemerera komanso chakasakaniza mamawa ndi madzulo uliwonse ndipo masana ndimazipatsa zakudya zamasamba. Sindiyiwala kuzipatsa madzi akumwa katatu patsiku komanso katemera wa njoka za m’mimba miyezi iwiri kapena itatu iliyonse. Ndimaonetsetsa kuti ikangoswa, pasadutse masiku 6 ndisadawapatse Vitamin ndi Iron komanso ndimawadula mano. Ndimatsetsa ndikukolopa m’khola kawiri patsiku kuti muzikhala mwa ukhondo.

Nanga chakudya cha kasakaniza mumachikonza bwanji?

Ndimasakaniza madeya, soya, chimanga ndi zothandizira kuti zizikula mwachangu.

Kodi matenda a chigodola omwe amapha nkhumba zambiri mumathana nawo motani?

Chiyambireni ulimiwu sindidakumanepo ndi matendawa chifukwa ndimakhwimitsa chitetezo ku makola anga kuti pasafike munthu wina aliyense, komanso sizituluka.

Nanga ndi mavuto otani omwe mumakumana nawo mu ulimiwu?

Vuto lalikulu ndikusowa kwa madeya makamaka m’nyengo ya mvula zomwe zimachititsa kuti tizimugula mokwera mtengo kwambiri. Vuto lina ndi kusowa kwa misika yogwirika bwino choncho ndimayenera kusaka ndikuzipangira ndekha msika komabe ndimayetsetsa kuti ndipitebe chitsogolo.

Kodi masomphenya anu ndi wotani?

Ndikufuna kutsogoloku nditamadzaweta nkhumba zokwana 3 000, komanso kukhala ndi mitundu ya makono ya nkhumba yomwe yangotuluka kumene. 

Nanga mlimi yemwe akufuna kuyamba ulimiwu mungamulangize zotani?

Choyambirira, afufuze misika, apeze upangiri wa momwe angawetere komanso njira zopangira chakudya chotsika mtengo. Chachiwiri, ayikepo mtima kwambiri pa ulimiwu ndipo asabwerere m’mbuyo akaona kuti penapake sizidayende bwino.

Related Articles

Back to top button
Translate »