Nkhani

Alimi akhutira ndi chionetsero

Listen to this article

Alimi ena amene afika ku chionetsero cha ulimi chimene nduna ya za malimidwe a Sam Kawale adatsegulira dzulo mu mzinda wa Blantyre ati akukhutira ndi chionetserocho.

Chionetserocho ndi cha nambala 19 ndipo chabweretsa pamodzi alimi, nthambi za boma, ogulitsa mbewu ndi zipangizo, mabungwe komanso makampani okonza katundu kuchokera ku za kumunda komanso ziweto ndi nsomba.

Mmodzi mwa alimiwo, mayi Alice Mbale ochokera ku Mafinga Irrigation ku Chisenga EPA m’boma la Chitipa adati apindula kwambiri chifukwa nthochi zonse zimene anabwera nazo zagulidwa ndipo ambiri akufuna kuti azilumikizana nawo pa nyemba zawo zimene amachulukitsa ndi kugulitsa kuti alimi akadzale.

“Ambiri akuchita chidwi ndi mbewu ya nyemba ya makono ya Nua 45 imene timachulukitsa kuti alimi akabzale. Mbewuyi ili ndi michere ya Zinc imene imathandiza kuti munthu aziona bwino komanso kwa amene ali ndi chilonda chimapola msanga,” adatero mayi wa ana anayiyo amene ali m’gulu la Tiyezge Seed Multiplication.

Mlimi wina, mayi Nancy Chidzalo wa ku HortiNet Foods Limited adati chionetserocho chathandiza kuti afikire misika ina ndi zimene amakonza kuchokera ku nthochi.

“Tikusanduliza nthochi n’kukonza banana crisps—tchipisi cha nthochi, komanso ufa wa nthochi. Ufawu timaukonza bwino. Zonsezi timazipakira bwino ndipo tikugulitsa kwambiri ku Lilongwe koma tsopano tifalikira madera enanso,” adatero iwo.

Ndipo mkulu wa bungwe la Centre for Agricultural Transformation (CAT) a Macleod Nkhoma adati adasangalala chifukwa abwera ku chionetserocho ndi alimi amene amagwira nawo ntchito m’dziko muno ndi ulimi wawo wosiyanasiyana.

“Tabwera ndi alimi amene akusanduliza zosiyanasiyana kuchokera kumunda. Ena akuchulukitsa mbewu. Komanso ena akukonza zakudya za nsomba zimene mmbuyomu alimi a nsomba amagula ku Zambia. Izi zithandiza kuti ndalama zizikhalira m’dziko momwe muno,” adatero iwo.

A Nkhoma adati iwo ndi wokondwa kuti bungwe lawo, lidapeza imodzi mwa mphoto 6 zimene zidaperekedwa ku chionetserocho.

Polankhula potsegulira chonetserocho, a Kawale adati padakalipano nkhani yoti ulimi ufike pena ngati bizinesi, ikadali mokwawa koma unduna wawo mogwirizana ndi magulu ena akuyesetsa kuti zinthu zipite patsogolo.

“Tikudziwa kuti makina othandiza kutukula ulimi ngokwera mtengo. N’chifukwa chake tikubweretsa njira zoti izi zisinthe kuti alimi aang’ono azitha kupeza makinawa bwino lomwe,” adatero iwo.

Chionetserocho, chimene chimachitika chaka ndi chaka chitha Loweruka ndipo chikuchitikira ku Chichiri Trade Fair Grounds mu mzinda wa Blantyre. Mutu wake ndi Kudzidalira potenga ulimi ngati bizinesi.

Related Articles

Back to top button