Nkhani

Alimi alirira Admarc

Lipoti la nthambi yochenjeza anthu za njala ya Famine and Early Warning Network (FewsNet) lati alimi a chimanga akupitirira kulira za mitengo yomwe akugulira chimanga chawo ndi mavenda chifukwa bungwe la Admarc lilibe ndalama.

Lipoti la FewsNet la August 2020 lati chifukwa cha vuto la ndalama ku Admarc komanso potengera kuti makampani opanga zinthu kuchoka ku chimanga achepetsa mlingo wa chimanga chomwe akufuna, alimi ena akugulitsa chimanga chawo  kunja kwa Malawi.

Kugula chimanga ku Admarc ndi ntchito yapadera

FewsNet yati mavenda ambiri omwe akugula chimanagacho akugula pamitengo yotsikitsitsa kuyerekeza ndi mtengo waboma wa K200 pa kilogalamu imodzi.

“Kupatula kuti alimi ambiri adakolola bwino, kwaoneka kuti makampani ambiri omwe amagula chimanga kuti azipangira zinthu achepetsa mlingo ndiye poti Admarc nayo ilibe ndalama, alimi akulowera  kulikonse komwe angamve msika,” latero lipoti la FewsNet.

Koma mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Frighton Njolomole wati zomwe zikuchitikazi zikuika dziko la Malawi pachiopsezo chokhala losowa chakudya chifukwa mmalo moti chimangacho chisungidwe ku nkhokwe zake, chikupita kunja.

“Ndondomeko yathu, timadalira kuti Admarc ikagula chimanga kwa alimi, imadzatigulitsa pa mtengo wabwino nthawi ya njala koma ngati Admarc siyikugula chimanga ndipo alimi akugulitsa kunja, njala ikadzabwera mayiko amenewo adzatigulitsa mokwera,” adatero Njolomole.

Iye adati poti alimi ena akadali nacho chimanga, boma lichite changa popereka ndalama ku Admarc kuti igule chimanga chomwe chatsalacho n’kusunga kunkhokwe kuti dziko likhale mpodalira kumbali ya chakudya.

Nduna ya zamalimidwe Lobin Lowe atayendera ntchito zamalimidwe ku Salima adati boma likukonza ndondomeko yodzutsira Admarc kuti alimi azipeza potsamira akakolola mbewu zawo ndipo akufuna kugulitsa.

“Kale mlimi amatha kudziwa ndalama zomwe adzapeze akadzakolola nkugulitsa mbewu zake chifukwa Admarc idali yamoyo ndipo mitengo imatuluka nthawi yabwino choncho, mlimi amatha kudziwa kuti ndikakolola zochuluka mwakuti, ndidzapeza ndalama mwakuti,” adatero Lowe.

Iye adatsimikiza kuti magulu aalimi akhala akupita ku likulu la undunawu kumakadandaula nkhani ya mitengo ya mbewu ndipo adati kulira kwa mtundu umenewu kwatsala pang’ono kutha chifukwa boma lidzutsa Admarc.

Boma likamapanga mitengo ya mbewu, limawerengera zomwe mlimi adalowetsa kuti atulutse kilogalamu imodzi ndipo limawonjezerapo kangachepe kuti kakhale phindu la mlimi kutanthauza kuti mavenda akamagula pamtengo osafika pa mtengo wa boma amakhala kuti akupha mlimi.

Kadaulo pa zamalimidwe Tamani Nkhono-Mvula adaunikirapo kuti mchitidwe uwuwu utabwerezedwa kwa zaka zingapo zotsatana, alimi ambiri akhoza kusiya ulimi chifukwa chosowa mpamba.

“Ngati mlimi ali ndi K1 miliyoni yomwe walowetsa muulimi ndipo chaka choyamba mavenda amubera K200 000 ndiye kuti watsala ndi K800 000. Pakutha kwa zaka zinayi akuberedwa K200 000 chaka chilichonse, mlimi adzakhala opanda ngakhale 1 tambala.

Iye adati mpofunika kuti boma libwezeretse Admarc momwe idalili kale pomwe inkagula chimanga ndi mbewu zonse kuchoka kwa alimi nthawi yabwino chifukwa inkakhala ndi ndalama ndipo alimi ankakhala ndichikhulupiliro kuti akagulidwa mbeu zawo ku Admarc.

Kadaulo pa za ndale Henry Chingaipe yemwe adachita kafukufuku wa ntchito ndi mavuto a Admarc mmalo mwa bungwe la Civil Society Agriculture Network (CisaNet) adapeza kuti bungwe la Admarc likhoza kugwira ntchito bwino litachoka mkhwapa mwa ndale.

Iye adati bungwe ngati la Admarc ndi ndale siziyenderana ndipo zikangololedwa kulowererana, ntchito za kampaniyo zimalowa pansi chifukwa atsogoleri ake amauzidwa zochita ndi andale omwe siziwakhudza ngati kampaniyo ikuyenda kapena ayi.

Mkulu wa kampani ya Admarc Felix Jumbe adati potengera momwe nkhokwe za m’dziko muno zilili, n’kulakwa kwakukulu kugulitsa chimanga kunja ngakhale kuti msika ukupezeka kunjako.

Pofika pa 5 August 2020, Admarc idali itagula matani 35 000 a chimanga pa mtengo wa K200 pa kilogalamu ndi ndalama zokwana K7 biliyoni yomwe idapatsidwa ndi thumba la ndalama za Malawi komanso idagula matani 20 000 owonjezera ndi ndalama zomwe idakongola ku mabanki.

Related Articles

Back to top button
WordPress › Error

There has been a critical error on this website.

Learn more about troubleshooting WordPress.