Nkhani

Amalawi alankhula: Masiku 30, boma liyankhe—Gift Trapence

Malawi adayaka moto dzulo m’zigawo zonse pamene anthu adayenda pokhumudwa ndi ntchito za boma la DPP.

Mfundo yamangidwa ndiyoti boma liyankhe m’masiku 30 apo ayi Amalawi abwereranso kumsewu.

Mmodzi mwa amene adakonza zionetserozo, Gift Trapence wa bungwe la Centre for the Development of People (Cedep), adati ayembekezera kuti boma liwayankhepasanathe masiku 30.

“Pali nkhani zambiri zomwe tikufuna boma liyankhe. Koma tawapatsa masiku 30 kuti akhale atayankha. Mfundo iliyonse yomwe tawalembera ili ndi nthawi yake koma nthawi yaitali pa zonse ndi masiku 30,” adatero, ndipo adaonjeza: “Ngati boma siliyankha, tiwauza Amalawi kuti tiyendenso”. Mumzinda wa Blantyre, Lilongwe, Zomba, Rumphi ndi Mzuzu, Amalawi adayenda pokapereka madandaulo awo kwa akuluakulu a boma.

Sadangoyenda, koma kuimba nyimbo zosiyanasiyana zomwe zidakutidwa ndi uthenga wodzudzula mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika komanso nduna zake.

Tichotse nkhalamba ndi mtima umodzi. Bewu—bewula Peter, bewula Chaponda, bewula Goodall komanso nyimbo ya Mukamva hi! Ho! agogo athawa ndi zomwe zidamanga nthenje.

Izitu zimachitika pamene amabungwe omwe si aboma, zipani zotsutsa komanso amipingo akhala akukakamiza mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti ayankhepo madandaulo awo.

Anthu akufuna Mutharika achotse nduna ya zachuma Goodall Gondwe komanso ya maboma ang’ono Kondwani Nankhumwa pokhudzidwa ndi nkhani ya K4 biliyoni yomwe imagawidwa kwa aphungu 86 zisadasinthe kuti ziperekedwa kwa aphungu onse.

Amabungwewa akuda kukhosi ndi boma pa nkhani ya kuzimazima kwa magetsi chikhalirecho boma lidagula majeneleta kuti lithane ndi  vutoli.

Mumzinda wa Blantyre, zionetsero zidayamba pa Kamuzu Stadium ndipo zidakathera ku khonsolo ya mzindawu komwe amabungwe adapereka kalata ya madandaulo awo kwa Charles Mphepo wa khonsoloyo.

Amene amatsogolera zionetserozo mumzindawu, Masauko Thawe adati maso ali pa boma. “Sikuti tasowa zochita, koma tikufuna boma lichitepo kanthu. Tikukhulupirira kuti boma liyankha,” adatero Thawe.

“Talandira ndipo tikutsimikizireni kuti uthengawu ufika kwa okhudzidwa,” adatsimikiza Mphepo.

Mumzindawu mudalibe zachiwawa chifukwa cha kuchulukwa kwa apolisi.

Muzinda wa Lilongwe, ziwawa zikadachitika chifukwa apolisi amakaniza anthu kuti akapereke madandaulo awo ku ofesi ya mtsogoleri wa dziko lino ndi nduna zake.

Mochedwa, apoliwo adaloleza kuti anthuwo akwawire kwa ndunako ndipo adakasiya madandaulo awo kwa mlembi mu ofesiyo, Cliff Chiunda.

“Musakaike, kalatayi ikafika kwa oyenerera,” adatero Chiunda.

Ku Mzuzu, zinthu zidathina pamene anthu ochita zionetserozo amang’amba mbendera za chipani cha DPP.

Izi zidatsutsula apolisi amene adathamangitsana ndi anthuwo. Moto udazirara pamene anthu adayendabe kukapereka madandaulo awo ku ofesi ya khonsolo ya mzindawo kwa MacLoud Kadam’manja.

Ena mwa odziwika amene adayenda nawo adali Harry Mkandawire, phungu wa ku mvuma kwa boma la Mzimba komanso Kamuzu Chibambo yemwe ndi mtsogoleri wa chipani cha Peoples Transformation Party (Petra).

Amene amatsogolera zionetserozo m’bomalo Charles Kajoloweka adati apereka masiku khumi kuti Gondwe ndi Nankhumwa achoke, komanso kuti wamkulu wa apolisi, Rodney Jose yemwe akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa Robert Chasowa achotsedwe.

Lachisanu, anthu a chipani cha DPP adayenda mumzinda wa Blantyre kuopseza aliyense amene ayenda kuti achita naye.

Komabe izi sizidalepheretse anthu ena kuphatikiza Daniel Phiri kutuluka m’nyumba zawo dzulo.

“Satana wachita mwanyazi. Ngati atsogoleri athu ali okumva ayankhe zomwe tawadandaulira. Mankhwala akusowa, magetsi kulibe, kodi tikhala bwanji?” adatero Phiri wochokera kwa Manase mumzinda wa Blantyre.

Related Articles

Back to top button