Nkhani

Amalawi okwiya asambwadza BBC

Lachiwiri pomwe timu ya dziko lino ya Flames inkakonzekera kukumana ndi Senegal mumpikisano wa matimu a mu Africa, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adalonjeza K1 miliyoni kwa amene alowe mkati ndi K500 000 kwa amene akhale pabenchi timuyo ikachita zakupsa.

A Chakwera adaponya uthenga wawo m’masamba a mchezo pofuna kulimbikitsa anyamatawo chifukwa Senegal ndi timu yomwe ili pamwamba pa matimu onse muno mu Africa.

Ataponya uthengawo, tsamba la mchezo la BBC News Africa pa Facebook lidaponya funso kufunsa omvera, oonera ndi otsatira tsambalo maganizo awo pankhaniyo chifukwa zimaoneka kuti uku n’kutaya ndalama.

Koma zotsatira zake, Amalawi adaponya ndemanga zoposa 7 000 m’maola awiri patsambalo ndipo ambiri adadzudzula tsambalo pofuna kulowerera pa zochitika za m’dziko muno. Chopatsa chidwi chidali choti ngakhale wailesiyo imalengeza nkhani zake zambiri m’Chingerezi ndi zilankhulo zina monga Chiswahili, Amalawiwo amayankha nkhaniyo m’Chichewa.

Poona ndemanga zambiri, zimaoneka kuti Amalawi adakwiya chifukwa zikuoneka kuti BBC imafuna kunena kuti mtsogoleri wa dziko linoyo adalonjeza ndalamazo pomwe zikadagwira ntchito zina zachitukuko osati kupereka kwa anyamata a mpira omwe amalandira kale malipiro.

Komatu akanadziwa sakanatero, chifukwa khamu lochuluka la Amalawi linayala mphasa pa tsamba lawo ndi kuwanyoza komanso kuwagemula mopanda chigamba. Ambiri mwa anthuwo amafuna kudziwa ngati panali cholakwika chilichonse mtsogoleri wa dziko lino kupereka mphatso kwa anyamatawo powalimbikitsa kuti achite bwino.

Mwa zina anthuwo omwe ndemanga zawo zinali zitadutsa 26 000 pofika Lachinayi, anauza wailesiyo kuti yasowa nkhani pomwe ena anaiuza kuti isamalowelere za m’nyumba mwa eni.

Ndemanga monga: “Zausatana, mwasowa zochita eti, mwatitokosola, mphuno ngati Rambo, mutu ngati madwale awiri,” zinamanga nthenje pa tsambalo.

Pomwe mtolankhani wa BBC Bora Mosulo anafunsa mafunso nduna ya zofalitsa nkhani m’dziko muno a Gospel Kazako za nkhaniyi, adamuyankha kuti ndi chikhalidwe cha Amalawi kupatsana mphatso ndipo panalibe cholakwika chilichonse ndi zomwe a Chakwera adachita.

Ndipo nkhaniyo siyinathere pomwepo chifukwa Amalawi ankhaninkhani adakhamukiranso ku nkhani zina patsambalo kuwauza a BBC kuti apepese ndipo ngati satero, Amalawiwo azigona patsambalo.

Pofika Lachinayi Amalawi anaonetsa kutsimikiza kwawo ndipo adalemba kalata yoti isainidwe ndi anthu 1000 yomwe itakakamize a BBC kuchotsa nkhani yonyanzitsayo pa tsamba lawo. Pakutha pa mphindi 30, kalatayo inali itasainidwa ndi anthu oposa 500.

Apa panapezeka Amalawi ena monga Mphatso Chidothe yemwe amatumiza kalata pa tsamba la BBC, koma mosakhalitsa Chidothe sadathenso kutumiza kalata zomwe zinangosonyeza kuti amutsekera panja ndipo sangathenso kutumiza kalatayo ngakhale amakwanitsa kulembapo zina zonse.

Polankhula ndi Msangulutso, Chidothe anati anakhumudwa ndi mchitidwe wa BBC wonyanzitsa Malawi.

“Ndinakhumudwa nditaona zomwe a BBC analemba zonyanzitsa dziko lino, komanso zomwe mtolankhani wawo analankhula ndi nduna ya zofalitsa nkhani a Kazako zosonyeza kuti chifukwa choti ndife dziko losauka ndiye kuti sitingapatsane mphatso zolimbikitsana mpaka kufunsa komwe ndalamazo zikuchokera, komanso a BBC titafika ndime ina sanalembe zomwe zikusonyeza kuti amalemba zoipa zokhazokha, zabwino ayi. Choncho tikufuna apepese,” anatero a Chidothe.

Iwo anafunsa kuti kodi poti Malawi ndi dziko losauka, sakuyenera kupatsana mphatso poonetsa chisangalalo chawo.

“Anthu osaina akakwana 1 000, tiwanenera ku Facebook ndipo zomwe alembazo zikhonza kuchotsedwa pa tsamba lawo,” anatero Chidothe.

Poikapo mlomo, mmodzi mwa akatakwe pa nkhani za zilankhulo m’dziko muno Jerome Chisikwa adati zachitikazi zikutanthauza kuti Amalawi anatha mantha ndipo akutha kudzilankhulira za momwe chitaganya cha lerochi chikuwaipira pogwiritsa ntchito chilankhulo chawo.

“Choncho polemba ndemanga m’zilankhulo zathu zikungosonyeza kuti ngati dziko tikupita chitsogolo potuluka zikhalidwe zathu,” anatero Chisikwa.

Pomwe katswiri wina kuchokera kusukulu ya University of Malawi a Charles Chilimampunga anati palibe cholakwika chomwe mtsogoleri wa dziko lino adachita polonjeza mphatso ku timu ya Flames chifukwa ndi chikhalidwe chathu kupereka kangachepe munthu akachita bwino.

Pa nkhondo ya pakati pa Amalawi ndi a BBC, Chilimampunga anati ndi nkhondo ya pakati pa olemera ndi osauka ndipo Amalawi angofuna kuonetsera poyera kwa BBC kuti ngakhale dziko lawo lili losauka, amachita ziganizo zawo zomwe olemerawo asamalowererepo.

“Amalawi anayankha mwa mkwiyo chifukwa pakadalipano akudutsa m’nyengo yowawa pa za chuma ndipo mpirawo ndi omwe ukubweretsako mpumulo ndi chisangalalo,” adatero a Chilimampunga.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button