Nkhani

Amayi abisa katundu wa K16 000 mu panti

Listen to this article

Ukathyali wakasololedwe wachitika pamalo omwetsera mafuta a Puma pa Wenela pomwe apolisi adanjata mkulu wina wa ku Zambia pomuganizira kuti amathandizira amayi awiri omwe akuwaganizira kuti amatulutsa katundu mushopu pomubisa kumalo obisika.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Blantyre, Yona Thembachako, watsimikizira Msangulutso za kunjatidwa kwa John Bwanga, yemwe akuti padakalipano amutumiza kwawo chifukwa adalibe zikalata zokwanira zomuyenereza kukhala m’dziko muno.

Malinga ndi Thembachako, ogwira ntchito m’shopumo amadabwa ndi kusowa kwa katundu wina koma osadziwa yemwe akuba. Iye wati izi zidachititsa ogwira ntchitowo kuti ayang’ane ma vidiyo kamera m’shopumo kuti aone chomwe chimachitika.

Thembachako wati ogwira ntchito pamalopo atayang’ana pakamera adaona amuna awiri akumatchingira mlonda yemwe ankalondera mushopumo pomwe amayi awiri akulowetsa katundu kumanyazi.

Wogwira ntchito wina mushopumo, yemwe sadafune kutchulidwa, wati tsiku loyamba amayiwo adatenga zitini ziwiri za mkaka wa ana zolemera magalamu 400 n’kuulowetsa m’madiresi.

Kenaka akuti adaonanso mayi akutenga chigubu cha mafuta ophikira cholemera malita 5 n’kuchipanira kumeneku.

“Atatero adatuluka panja pomwe padali galimoto ndi diraiva wawo ndi kuuyatsa,” adatero iye.

Iye adati adadabwa ndi momwe amayiwa amalowetsera katunduyo pakati pa miyendoyo.

“Amangokweza diresi n’kupanira katunduyo. Pomwe amalowetsa zitinizo m’mphechepeche zimaoneka koma komwe kumalowa katunduyo ndiye sikumaoneka,” adatero kufotokoza zomwe zimachitika pa 27 April.

Akuti katunduyo adali wa ndalama zokwana K15 955.

Atazindikira izi akuti adakhala mochenjera ndipo pa 5 May adabweranso. Patsikulo akuti adatenganso mowa wa Carlsberg Green ndi mpunga wolemera makilogalamu asanu. Sadadziwe kuti la 40 lakwana!

Ogwira ntchito mushopumo akuti adali tcheru malinga ndi zomwe adaona pa vidiyopo kuti akaona anthu ofanana ndi amenewo achenjere nawo.

Patsiku logwidwali anthu ogwira mushopumo atamuwona Bwanga adatseka pakhomo ndi kumugwira ndipo adamutengera kupolisi ya Blantyre komwe apolisi adamusunga kuti amufufuze.

Thembachako wati Bwanga adavomereza kuti ndi iyeyo amene akuoneka pavidiyopo koma adati amayi enawo adangokumana nawo momwemo.

Bwanga akuti adatinso mayi mmodziyo ndi nzika ya ku Zambia.

Thembachako akuti Bwanga adakana mlandu woti amathandizira kapena kuba nawo katundu.

“Titamufunsitsitsa mpomwe tidapeza kuti alibe ziphaso zokhalira m’dziko muno ndiye a ku ofesi ya Immigration adamutumiza kwawo.

“Ndi zoonadi kuti akadatithandiza kafukufuku wa amayiwo koma timawona kuti tikungomusunga woti adakana za nkhaniyo,” adatero Thembachako, yemwe adati apolisi akufufuza ndi kusakasaka amayiwo ndi mwamuna yemwe akuwoneka pavidiyopo.

Related Articles

Back to top button
Translate »