Nkhani

Amayi chepetsani zotsirana phalazi

Listen to this article

Kawirikawiri nkhani ya nkhanza za m’mbanja imagonera abambo kuti ndiwo ali patsogolo kuzunza amayi.

Tikaonetsetsa chiwerengero cha nkhanza za m’banja chikutero ndithu,  koma amayi nawo alowa chisimo chokhuthulira abambo phala kapena madzi amoto akawakwiyitsa.

Sindikufuna kuchepetsa nkhanza zomwe amayi akukumana nazo, koma kuti mwina titaunikanso mbali yomwe amayi sakuchita bwino chifukwa nthawi zina poima pa zowawa zomwe amayi akudutsamo tidzayamba kuiwala abambo ena omwe aphedwa komanso kuvulazidwa ndi amayi.

Zokwiyitsa kapena kusamvana sikungalephere pamene pali  anthu awiri. Kusemphana maganizo kapena zochita ndiye umunthuwo chifukwa palibe angaganize mofanana ndi mnzake nthawi zonse. Iyi ndi mbali imodzi ndithu yamoyo.

Koma chimene chimativuta anthu ndi kulephera kuugwira mkwiyo nkupeza njira za mtendere zothetsera kusamvana.

Zilibe kanthu kuti kaya wakunamiza bamboyo; kaya wapeza chibwenzi; kaya wachimwitsa mayi wina; palibe choyenereza mayi kuti atenge phala lamoto kapena madzi owira nkumukapiza nawo. Mtima ofuna kumuvulaza wina motere ngwa nkhanza zoopsa.

Ngati sunagwirizane ndi khalidwe wa bamboyo komanso ngati kukambirana kwavuta, ndi bwino kutsanzika kuti mulekane mwamtendere kusiyana ndi kuti wina azunzike ndi mabala, zipsera kapena zilema chifukwa choti mkazi wake adakwiya zedi.

Pambali pongovulaza, mchitidwewu ukhonzanso kupha munthu wabamboyo. Ndithu munthu akalowe m’manda mwa njira iyi chifukwa mayi anakwiya?

Mumphindi zochepa za mkwiyo  maganizo amgwazo akuti ‘ndimkhaulitse amaneyu’ akhoza kusokoneza miyoyo yambiri .

Pamene bambo ovulazidwayo ali kuchipatala, mayi wolakwayo amakhala mmanja mwa apolisi kudikira kuti azengedwe mlandu omwe kawirikawiri amakathera nawo mdende.

Nanji akamwalira bamboyo, pamene akukalowa mmanda zimadziwikiratu kuti mayiyo yakenso ndi ndende yamuyaya. Ovutika poterepa amakhala ana, makolo okalamba komanso ena omwe amadalira awiriwa pachithandizo cha moyo wawo.

Pamene amayi tikudandaula za nkhanza zomwe timakumana nazo m’mbanja, tisaiwale kuti nafe tili ndi udindo oonetsetsa kuti tisachitire ena nkhanza. Kaya walakwa bwanji bamboyo palibe chifukwa choti akapizidwe madzi amoto.

Related Articles

Back to top button
Translate »