Nkhani

Amayi oyendayenda akanizana migodi

Listen to this article

Amayi oyendayenda sakumwera madzi chitsime chimodzi m’boma la Ntchisi polimbirana migodi.

Nkhaniyi ikuti pali gulu la amayi achichepere ogulitsa matupi awo m’malo azisangalalo m’bomalo lomwe likumathamangitsa ndi kunyoza amayi okulirapo misinkhu kuti awalekere migodi yawo.

Wapampando wa amayi oyenendayenda m’bomalo a Legester Chimkanda anatsimikiza kuti mikanganoyi yomwe ndi ya pa kanthawi yafika povuta m’bomalo.

Iwo anati chifukwa cha kutopa ndi mtudzu, ndewu ya mnanu inabuka Lamulungu yomwe inasiya amayi 5 atabaidwa ndi mabotolo, katundu kuonongedwa pomwe amayi ena awiri omwe ndi achichepere komanso apachibale ali m’manja mwa apolisi.

“Gwero la nkhaniyi ndi yoti amayi achicheperewa akumanyoza anzawo achikulire akapeza mphongo, kwinaku akuiseka mphongo ija kuti yatenga mayi wachikulire kusiya achichepere,” anatero a Chimkanda.

Iwo anati pali chiopsezo kuti ngati nkhanizi siziunikilidwa bwino, ena akhoza kutayapo miyoyo.

Ndipo pakadalipano, apolisi m’bomalo alowererapo pokhazika pansi mbali ziwirizo.

Pomwe mneneri wa polisi m’boma la Ntchisi a Yohane Tasowana anatsimikiza kuti anatsekera a Anastanzia Banda a zaka 22 komanso Janet Banda a zaka 19 powaganizira kuti anabaya anzawo ena asanu ndi mabotolo a mowa.

Iwo anati magulu awiriwa akhala akumenyana chifukwa cholimbirana amuna kwa miyezi ingapo tsopano.

“Milandu ya magulu awiriwa yakhala ikutipeza ku polisi kuno ndithu,” anatero a Tasowana.

A Tasowana anati amayi apachibalewo, anapeza mphongo zomwe anagwirizana nazo ndipo ali paulendo wopita ku malo ogona alendo anakumana ndi amayi ena 5 omwe anawakaniza amayi awiriwo kutengana ndi mphongozo.

“Izi sizidakomere amayi a pa chibalewo ndipo ndewu yoopsa inabuka pamalopo,” anatero a Tasowana.

Iwo anati amayi apachibalewo anabaya amnzawo asanuwo ndi mabotolo ndi kuvulaza atatu mwa iwo kwambiri.

A Tasowana anati amayi a pachibalewo omwe amachokera m’mudzi mwa Maunde, Mfumu Tambala, m’boma la Dedza, awatsekulira milandu yovulaza anthu.

Iwo anati amayi ovulazidwawo anathamangira nawo kuchipatala cha Ntchisi komwe anakalandira thandizo la mankhwala. n

Related Articles

Back to top button