Jannah Theme License is not validated, Go to the theme options page to validate the license, You need a single license for each domain name.
Nkhani

Ana 1 487 abadwa pa Khrisimasi

Ku Dowa kudabadwa ana 71 tsiku la Khrisimasi chaka chino. M’dziko lonseli mudabadwa ana 1 487 pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Yesu Khristu.

Choncho, n’zochititsa chidwi kuti mmodzi mwa ana amene adabadwa tsikulo, ku Dowako, adapatsidwa dzina ndi mtsogoleri wa chipani cha UTM, a Dalitso Kabambe.

Lidalitu tsiku la chimwemwe kwa mayi Charity Billy pa chipatala cha Mponela m’boma la Dowa. Chimwemwecho chidasefukira a Kabambe atafika pa chipatalapo kukachereza odwala.

Mayi Billy adakuwira a Kabambe kuti amutchule mwanayo dzina.

“Nditawaona, ndidakumbuka ntchito za chifundo zimene akhala akumveka nazo. Pomwe amupatsa mwanayu dzina lawo, pali kuthekera kwakukulu kuti akhoza kudzachita bwino ngati mmene alili eni dzinali,” anatero mayiwo.

Patsikulo, a Kabambe adachereza odwala m’zipatala za Mponela, Madisi, Kasese ndinso Kabudula ku Dowako.

Ndipo atatcha dzina mwanayo, a Kabambe adati izi zikutanthauza kuti iwowa adzatengapo gawo lomusamalira mnyamatayo.

“Ndikhalirana pansi ndi a ku nyumba kwanga kuti tigwirizane za mmene tingathandizane nawo makolo a mwanayu pa kumulera,” adatero a Kabambe.

Iwo adati akufuna kuti mwanayu akule akudziwa makolo ake enieni komanso akudziwa banja la a Kabambewo monga makolo akenso.

Ana 1 487 ndiwo adabadwa pa tsiku la Khrisimasi m’dziko lino, poyerekeza ndi 1 462 amene adabadwa pokumbukira tsiku la kubadwa kwa Yesu Khristu chaka chatha.

Chiwerengero chochokera ku unduna wa za umoyo chasonyeza kuti mwa ma Christmas Baby a chaka chinowa, 764 ndi aakazi ndipo 723 ndi aamuna.

Lilongwe ndiye yadya wani ndi makanda 244 ndipo Blantyre ndi yachiwiri ndi ana 109. Mangochi, imene idatsogola chaka chatha ndi makanda 89, chaka chino kwabadwa ana 97. Ku Kasungu kwabadwa ana 76, Dowa 71, Mulanje 65 ndi Zomba 63. Likoma komwe kwabadwa mwana mmodzi ndi boma lomwe lili ndi chiwerengero chotsikitsitsa mwa maboma 28 a m’dziko muno.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button