Nkhani

Ndalama zawo sizikulondeka

Zikomo,

Anatche, ine zandivuta koopsa. Ndili pa banja ndipo ndili ndi ana atatu.

Banja lathu ndi losalongosoka. Ndanena chonchi chifukwa amuna anga satha kusamala banja.

Amagwira ntchito ndipo amalandira ndalama zambiri. Sanandiuzepo ndalama zomwe amalandira koma nthawi yinayake ndinaona payslip yawo. Ndinadabwa kuona ndalama zomwe amalandira.

Ife timangoti takhala apa takhala apa chifukwa choti satha kulipira lenti. Kuti agule zakudya pakhomo zimawavuta. Ndi bambo uja opanda manyazi. Amatha kundiuza kuti pita ukapemphe ufa ndi ndiwo kwa anzako.

Anthu akwathu anatopa nawo ndi kupempha. Ndiye ali ndi chiwanda chokongola ndalama koma osabwenza.

M’nyumba mwathu katundu ndi woti abale anga adatipatsa. Iwo amatha kutenga katundu wa nyumba ndi kukagulitsa kuti apeze thiransipoti yopitira ku ntchito.

Chodabwitsa n’choti samwa mowa koma amabwera mkati mwa usiku. Kuwafunsa komwe amakhala ndi komwe ndalama zawo zimapita, sayankha zonveka.

Ana athu amakhalira kundifunsa kuti kodi adadiwa amagwiradi ntchito? Nanga ndalama zao zimapita kuti? Pakhomo pathu ndi pakhomo pomvetsa chisoni.

Ana amalakalaka nyama koma abambowa sagula.

Ku mpingo wawo ndi munthu wodalirika zedi, ndipo ooneka okhulupirika.

Anatchereza, ndatopa ndi mavuto a pa banja pangapa. Ndikamawaona ana anga akuvutika chonchi ndimasautsika mumtima mwanga kwambiri.

Kwakhoswe ndiye anatopa nafe koma samasintha. Ndipo safotokoza komwe kumapita ndalama zao.

Abambowa adandipeza ndikugwira ntchito koma anandisiyitsa.

Nditaine ine Anatche?

Nadzimbiri.

Anadzimbiri,

Muli pa mavuto kwambiri. Vuto loyamba ndi loti mumadziwa ndalama zomwe amuna anu amalandaira. Komanso vuto lina ndi loti amuna anu samwa mowa.

Abambo amenewatu mwina mutu wawo siugwira. Ali ndi chibwana kwambiri. Sangamasiye ana pakhomo opanda chakudya.

Analakwitsa kukusiitsani ntchito. Lero ndi izi zikumuvuta kudyetsa pakhomo ndi kulipira lenti. Mwamuna wachibwana. Zimakhala zochititsa manyazi ngati mukukanika kupereka lenti ndi zinthu zina.

Poti kwa a nkhoswe zakanika, pitani ku mpingo mukadandaule. Mukafotokoze za khalidwe lawo lonse kuti akuthandizeni.

Mufufuzenso kuti chikhalidwe chawo chinali chotani adakali ang’ono. N’kutheka kuti munthuyo ndi wa umbombo kwambiri. Alipotu abambo ena ambombo osatha kudyetsa ana awo omwe. Anthu amenewa zimawavuta kusamala pakhomo.

Ine ndikuona kuti muyambe kufunafuna ntchito. Ndipo ikapezeka kayambeni. Mmene mukukhaliramu amuna anu sangathe kusamala banja ngati sasintha khalidwe lowolo.

Anatchereza.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button