Chichewa

Anatchereza

Ndili pa moto

Gogo,

Ndili pa ubwenzi ndi mtsikana wina yemwe amaphunzitsa pa sukulu ina ya pulayimale ya mu mzinda wa Blantyre.

Ndimamukonda nayenso amaonetsa kuti amandikonda.

Koma chimufunsirire, ndikusowa mtendere chifukwa cha kuchuluka kwa zofuna zake.

Pang’onong’ono umva nditumizire mayunitsi a foni. Ndikatumiza, umva nanga zakonzetsera tsitsi?

Nthawi pang’ono umva kwathu aphika nyemba sindikuzifuna, nditumizire ndalama ndigule kanyenya wa nkhuku.

Gogo, ndisaname ndili pa moto ndi mtsikanayu chifukwa zofuna zake zikudutsa malipiro anga a pa mwezi moti ndayamba kulowa mu ngongole.

Kodi kukhala pa chibwenzi ndi choncho?

BHK

BHK

Mmbuyomu tidakhudzanso nkhani ngati yomweyi patsamba lino.

Anyamata ambiri amadandaula kaamba ka kuchuluka kwa zofuna za atsikana.

Atsikana ambiri akapeza chibwenzi amaona ngati apeza mgodi wa ndalama kuiwala kuti naye bwenzi lawo amapeza ndalama movutikira.

Izi zimachitita anyamata ambiri kusowa mtendere, komanso kugwa mu ngongole zoposa misinkhu yawo.

Ndikudziwa kuti ndinu wokhumudwa, koma kambiranani ndi bwenzi lanuyo kuti mumvetsetsane.

Mufotokozereni kuchuluka kwa ndalama zomwe mumapeza, zinthu zomwe mungakwanitse komanso zomwe simungakwanitse.

Ndikukhulupirira kuti amvetsetsa.

Natchereza

Ndapeza mkazi

Gogo Natchereza,

Ndikufuna ndithokoze kaamba koti ndapeza mkazi yemwe ndikuyembekezera kumanga naye banja.

Chaka chatha ndidapempha kuti mundisindikizire kalata yanga momwe ndidalemba kuti ndikufuna mkazi.

Mwachisomo cha Mulungu mkaziyo ndidamupezeka moti tikuyembekezera kuchita chinkhoswe masiku akudzawa.

Pitirizani kutitumikira, komanso kutipatsa uphungu.

GGH

GGH,

Ndine wokondwa kuti tsamba lino likupindulira awerengi athu.

Chokondweretsa kwambiri n’choti Mulungu kudzera patsamba lino adakwaniritsa chosowa chanu.

Ndikufuna ndipempha kuti mugwiritsitse m’dalitso womwe mwapeza chifukwa ngakhale Baibulo limati wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino.

Mulungu akudalitseni ndi kupitiriza kukwaniritsa zosowa zanu.

Natchereza

Related Articles

Back to top button