Nkhani

Anthu ambiri sakupita kukatsimikiza maina

Listen to this article

Ntchito yotsimikiza maina m’kaundula wa zisankho za chaka cha m’mawa ili pendapenda kaamba koti anthu ambiri saonetsa chidwi chopita kukaona maina awo.

Bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) latsimikiza kuti m’maboma momwe ntchitoyi yayamba monga Ntchisi ndi Dedza ndi anthu ochepa omwe apita kukatsimikiza maina awo m’kaundulamo.

Ena mwa anthu omwe adapita kukaona maina awo m’kaundula wa zisankho

Anthu ena akuti sadalandire uthenga uliwonse woti apite akatsimikize maina awo m’kaundulamo, koma National Initiative for Civic Education (Nice) Trust yatsutsa za nkhaniyi.

Mkulu wa Nice Trust, Ollen Mwalubunju, wati bungwe lake lakhala likufalitsa uthenga kudzera pa wayilesi, m’matchalitchi, m’misonkhano, komanso pogwiritsa ntchito galimoto zokuza mawu zomwe zimazungulira m’maboma momwe ntchito yotsimikisa maina ikuchitika.

“Ntchito yathu n’kuphunzitsa anthu za ndondomeko za chisankho moti momwe tidangoyamba kalembera mpaka pano sitidakhale pansi tikumema anthu kuti akatsimikize ngati maina awo ali m’kaundula wa zisankho,” watero Mwalubunju.

Ngakhale zili choncho, masiku oyambirira antchitoyi anthu ochepa ndiwo amafika m’malo momwe adalembetsera zisankho kuti atsimikize ngati maina awo akupezeka m’kaundula.

Mwachitsanzo, pa sukulu ya pupayimale ya Mlanda ku Dedza kudafuka anthu anayi okha kudzaona maina awo m’kaundula tsiku loyamba la ntchitoyi pa December 10 2018.

M’boma la Ntchisi m’malo ambiri anthu okaona maina samafika 30, kupatula kuchepa kwa uthenga, mkulu yemwe akuyang’anira ntchitoyi pa sukulu ya pulayimale ya Ntchisi, Helix Solomon, wati mvula ndiyo idalepheletsa anthu ambiri kukaona maina awo m’kaundula.

“Anthu ena akuti sadalandire uthenga uliwonse woti akatsimikize ngati maina awo ali m’kaundula wa zisankho. Ena akutangwanika ndi ntchito zakumunda pamene ena ikuwatsekereza ndi mvula,” watero Solomon.

Mneneri wa bungwe MEC, Sangwani Mwafulirwa, wapempha anthu kuti akaone maina awo komwe adalembetsera zisankho.

Mwafulirwa wati aliyense wofuna kusintha malo woponyera voti akafotokozera akuluakulu amalo womwe adalembetserawo kuti amuthandize kusamuka.

“Kukaona maina ndi bwino chifukwa aliyense yemwe adataya chitupa chake akapatsidwa mwayi wotenga chitupa china chatsopano bola akhale ndi umboni wokwanira, komanso dzina lake lipezeke m’kaundulamo,” watero Mwafulirwa.

Mkuluyu wati aliyense yemwe sadalembetsa m’kaundula nthawi ya kalembera sapeza mwayi wolembetsa pa nthawi yoona maina.

Zipani za ndale zosiyanasiyana zati zili pakalikiliki kumema anthu kuti akaone maina awo m’kaundula n’cholinga choti ngati pali kusokonekera kulikonse, akonzeretu kuti asadzakhumudwe tsiku loponya voti.

Mneneri wa chipani cha Malawi Congress (MCP), Maurice Munthali, wapempha aliyense wotsatira chipanicho kuti akatsimikize ngati dzina lake lili m’kaundula wa zisankhozo.

Naye mneneri wa chipani cha United Democratic Front (UDF) Ken Ndanga, komanso wa United Transformation Movement (UTM) Joseph Chidanti Malunga alankhula chimodzimodzi.

“Sitikufuna kuona zomwe zidaoneka pa kalembera moti pano tili mkati momema anthu kuti azikaona maina awo m’kaundula. Tifikira paliponse kufotokozera anthu za ubwino wokaona maina awo m’kaundula wa zisankho,” watero Munthali.

Ntchitoyi Ili m’magawo anayi ndipo gawo loyamba lidayamba pa 10 December ndipo litha dzuro m’maboma a Dedza, Lilongwe, Ntchisi, Dowa, Salima, Mchinji ndi Nkhotakota. n

Related Articles

Back to top button
Translate »