Aphunzitsi akhala ndi khonsolo
Unduna wa za maphunziro wati ukufuna kukhazikitsa khonsolo ya aphunzitsi yoti izikhazikitsa mwambo komanso kutukula ntchito yauphunzitsi.
Nduna ya za maphunziro Agnes NyaLonje adalengeza izi Lachitatu atatsegulira msonkhano waukulu wokumbukira aphunzitsi komanso sabata yolimbikitsa kuwerenga.
Iye adati iyi ndi imodzi mwa njira zomwe boma la Tonse Alliance likufuna kugwiritsa ntchito potukula ntchito za uphunzitsi.
“Boma la Tonse Alliance likufuna kuti aphunzitsi azitakasuka pantchito yawo chifukwa amagwira ntchito yaikulu. Mwaichi, tikukonza zokhazikitsa khonsolo ya aphunzitsi yoti izikhazikitsa mwambo,” adatero NyaLonje.
Koma bungwe la aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM) lati silinganenepo kaye kanthu paganizo la bomalo mpaka litamvetsetsa zomwe boma likutanthauza.
Mlembi wamkulu wa bungwe la TUM Charles Kumchenga wati mpofunika kumvetsetsa pomwe zizisiyana mphamvu ndi ntchito za khonsoloyo ndi za TUM.
“Kodi khonsoloyo udindo wake ndi wotani? Zikhonza kusokoneza kuti udindo wake ulowererane ndi wa TUM,” adatero Kumchenga.
Bungwe la TUM limayang’anira aphunzitsi powayimirira makamaka pa nkhani zokhudza madandaulo awo monga kuchedwa kapena kuduphadupha kwa malipiro, kuchedwa kukwezedwa pantchito ndi mavuto ena.
Padakalipano bungwe la TUM likuyimirira aphunzitsi pa nkhani ya ndalama za ukadziotche zomwe aphunzitsi akuti akuyenera kumalandira kaamba kophunzitsa m’nyengo ya Covid-19.
Nthambi zina monga za zachitetezo ndi umoyo, ogwira ntchito amalandira ndalama zaukadziotche zomwe ena zimafika K50 000 pa mwezi.
Pofotokoza bwinobwino za lingaliro la bomalo, NyaLonje adati ntchito yaikulu ya khonsolo ya aphunzitsi idzakhala yokhazikitsa mwambo pa ntchito yophunzitsa.
NyaLonje adatinso boma likukonza ndondomeko yokwezera aphunzitsi m’maudindo polingalira kuti chikwezereni aphunzitsi 25 000 chaka chatha, mipata yambiri ikadali yosatseka.
“Kukweza aphunzitsi tikweza koma zitengapo nthawi chifukwa tikufuna ndondomeko yabwino osati zongoti chulukechuluke ngwa njuchi ayi chifukwa zimapweteketsa ena,” adatero NyaLonje.
Iye adati boma likufuna kuti aphunzitsi azikwera potengera mbiri yawo yauphunzitsi pofuna kuchepetsa mchitidwe oti ena omwe agwira ntchito zaka zochepa azipezeka kuti akwera pomwe ena omwe agwira zaka zambiri ali pamodzimodzi.