Nkhani

Apolisi sakununkha kanthu pa chitetezo

Listen to this article

Ng’ombe zayang’ana kudazibomu!

Ubale wa anthu ndi apolisi wafika pa wa mphaka ndi galu moti apolisi sakununkhanso kanthu pa ntchito yawo yoteteza anthu ndi katundu wawo.

Asirikali a Malawi Defense Force kusungitsa mtendere pa zionetsero

Sabata zitatu zapitazo agogo 6 adaphedwa m’boma la Karonga powaganizira kuti ndi athakati.

Apolisi atapita kuti akagwire anthu omwe adachita izi, adawathamangitsa ndi miyala, mipini, mipaliro ndi zibonga moti adalephera kukwaniritsa zolinga zawo.

Aka sikadali koyamba izi zichitike m’bomalo. Chaka chathachi apolisi kwa Nyungwe adamenyedwa ndi anthu atatsekera anthu omwe adakatenga namulondola kuti adzawathandize kugwira mfiti m’deralo.

Nako ku Ntchisi anthu okwiya adapha agogo awiri powaganizira kuti adalodza mnyamata wina wa zaka 15 m’matsenga.

Ngakhale izi zidachitika mwezi wa October chaka chatha, mneneri wa polisi m’bomalo Richard Kaponda wauza Msangulutso kuti mpaka lero palibe yemwe wamangira mokhudzana ndi nkhaniyo.

Nako ku Neno komwe anthu adapha nkhalamba zomwe amaziganizira kuti ndi mfiti, apolisi adachita chidodo kuti akagwire ndi kuzenga mlandu anthu omwe adachita izi.

Anthu adali ndi mkwiyo waukulu moti apolisi amachita mantha kuti awagwire.

Nazo zionetsero zosonyeza kukwiya ndi momwe bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lidayendetsera chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino zaikanso pambalambala kufooka kwa apolisi moti boma lidapempha asirikali a nkhondo a Malawi Defense Force (MDF kuti awathandize kuteteza anthu ndi katundu wawo.

Mkulu wa apolisi Duncan Mwapasa adavomera pa msonkhano wa atolankhani kuti apolisi ali ndi mphamvu zochepa ndipo sangakwanitse kuteteza anthu omwe akuchita zioneserozo.

Apolisi akhala akuona mbwadza pa zionetserozo. M’malo moti apolisi azisaka amtopola, anthuwo ndiwo akumasaka apolisi n’kumawavula, kuwamenya, kuwalanda mfuti, kuwatsatira m’makomo n’kukachita chipongwe mabanja awo moti wapolisi wina, Imedi Usumani, adaphedwa.

Kuphwando la kumapeto a chaka chino, mkulu wa apolisi wa m’chigawo chakummwera Sladge Yousuf adati ntchito yoteteza anthu ikuvuta kaamba kakusakhulupirirana pakati pawo ndi anthu akumudzi.

Yousuf adati chodandaulitsa kwambiri ndi kuphwanyidwa, komanso kuotchedwa kwa mapolisi m’dziko muno.

Amalawi okwiya akumatsatira munthu yemwe ali mchitokosi mpaka kukaphwanya kapena kuotcha polisi n’kumutulutsamo.

Nkhamenya ku Kasungu ndi Chilobwe ku Blantyre ndi ena mwa mapolisi omwe adaphwanyidwa kaamba kosemphana Chichewa pakati pa apolisi ndi anthu akumudzi.

M’modzi mwa aphunzitsi a pa sukulu ya ukachenjede ya University of Livingstonia George Phiri adati apolisi asuluka chifukwa cha katangale, komanso utsogoleri wa dziko lino omwe wakoledzera moto kuti ntchito.

Phiri adati kwakhala kukutuluka malipoti ambiri a katangale yemwe apolisi amachita zomwe zamachititsa kuti Amalawi asowe chikhulupiriro mwa apolisi.

“Tsopano nkhani za katangale zonsezi zikatuluka, tikuona kuti palibe chomwe atsogoleri akuchitapo pofuna kuthana naye. Pachifukwa ichi anthu angoganiza zotengera malamulo m’manja mwawo,” iye adatero.

Phiri adati pakadali pano n’zovuta munthu kuthawira ku polisi kuti ukapezeko chitetezo chifukwa anthu akakwiya, akumathamangitsa omangidwayo komanso apolisi omwe akumuteteza.

“Atsogoleri a dziko lino akufunika kuti apeze njira zobwenzeretsa chikhulupiriro cha anthu mwa apolisi,” iye adatero.

Mwapasa atakumana ndi aphungu a chizimayi a ku Nyumba ya Malamulo pa nkhani yoti apolisi ena adagwiririra amayi ku Mpingu, Msundwe ndi Mbwatalika ku Lilongwe, adavomera kuti pali kusakhulupirirana pakati pa apolisi ndi anthu ndipo ayetsetsa kubwezeretsa chikhulupiriro mwa anthu pogwira ntchito mwachilungamo.

Related Articles

Back to top button