Atsogoleri a ndale akuona 2020 owala
Atsogoleri a zipani za ndale zomwe zidalimbana kwambiri pachisankho cha pa May 21 2019 ati akuona chaka chowala cha 2020 muuthenga wawo wotsekera chaka cha 2019 chomwe chatha mkati mwa sabata ikuthayi.
Uthengawu wabwera pomwe atsogoleriwa akudikirira zotsatira za mlandu wachisankho womwe akhala akukwekwesana kwa miyezi 7 tsopano.
Saulos Chilima wa UTM Party ndi Lazarus Chakwera wa Malawi Congress Party (MCP) adakokera kukhoti Peter Mutharika wa Democratic Progressive Party (DPP) pamlandu woti adabera chisankho.
Ubale wa atsogoleriwa wakhala wa khambi mpaka otsatira zipani zawo nawo adasanduka adani moti m’chaka cha 2019, m’dziko la Malawi mwakhala mukuchitika zipolowe.
Koma pomwe anthu nkhawa idakula kale kulingalira zotsatira za kukhoti, atsogoleriwa auza Amalawi kuti chomwe angachite n’kuchilimika pa ntchito chifukwa iwo akuona 2020 owala.
Muuthenga wake, Chakwera watsindika kuti 2020 akuoneka ngati ziyangoyango chifukwa cha mabala a 2019 koma Amalawi akapanga za nzeru, dzikoli lili ndi tsogolo lowala.
“Ngati mukuona mavuto onsewa, n’chifukwa choti mwakwera sitima yomwe woyendetsa alibe ukadaulo. Mu 2020 ndikudzipereka kukuyendetsani kuti mukafike bwino,” watero Chakwera.
Iye walozapo kufooka kwa ntchito zaumoyo kaamba kakuba mankhwala ndi zipangizo za chipatala, ngozi za pamsewu zomwe wati zikadatha kupeweka pakadakhala ngwiro pakati pa ntchito yokonza misewu, kufa kwa mafakitale ndi kulowa pansi kwa ntchito zamalonda.
Naye Mutharika watsimikizira Amalawi kuti zinthu zikuyenda bwino ku mbali yachitukuko ndipo walonjeza kuti mu 2020, Amalawi alandira zitukuko monga sukulu 250 000, tauni yamakono ku Mangochi ndi ntchito zotukula magetsi.
“Takonza zitukuko zambiri mu 2020 ndipo anthu aona kusintha. Mchaka chikuthachi, zinthu zidasokonekera chifukwa cha anthu ena omwe amafuna kubweretsa chisokonezo koma sizitheka,” adatero Mutharika muuthenga wake.
Chilima yemwe uthenga wake udali waufupi kwambiri pa onse adafunira Amalawi chaka cha 2020 chopambana ndipo adawalimbikitsa kuti apitirize kuchilimika popanga zinthu.
“Tiyeni tigwiritsitse umodzi womwe tidaonetsa mu 2019 kuti tipite chitsogolo ndi chiyembekezo chowala,” adatero Chilima.
Kadaulo pa ndale George Phiri wa ku University ya Livingstonia wati uthenga oterewu ndi wopereka chiyembekezo kwa Amalawi makamaka potengera kuti ukuchokera kwa atsogoleri awo.
Iye wati mtima omwe uli mwa atsogoleri ukadaonetsedwa mmbuyomu, zinthu zina zomwe zidasokonekera sizikadafika pomwe zidafikapo.
Khoti likuyembekezeka kupereka chigamulo cha mlandu wazisankho ndipo nkhawa ya Amalawi ochuluka ili pazochitika chigamulocho chikadzaperekedwa.