2019 Polisi Idaziona

M’chaka changothachi cha 2019, nthambi ya chitetezo ya polisi idalibe mpata opumira chifukwa cha mpungwepungwe womwe udalipo ndikusukuluka kwa chikhulupiliro pakati pa apolisi ndi anthu.

Ngakhale wogwirizira mpando wa mkulu wapolisi Duncan Mwapasa wavomereza izi muuthenga wake wotsanzikana ndi chaka cha 2019 chomwe Amalawi sadzayiwala m’mbiri ya dziko lino.

Mwapasa: Kudali mkokemkoke

Mwapasa wati ngakhale nthambiyo yayesetsa mbali zina monga kuchepetsa ngozi za pamsewu ndi anthu omwalira pangozizo, nkhani yokhazikitsa bata ndi mtendere udali mtunda ovuta kukwera.

“Zonse zidayamba bwino mu January ife n’kumati zili bwino koma atsogoleri awiri atangotsutsa zotsatira za chisankho cha mu May, 2019, kudali mkokemkoke ophwanya malamulo n’kutengera zonse m’manja mwa anthu,” adatero Mwapasa muuthenga wake womwe adaupereka pa 31 December 2019.

Iye wati apolisi ambiri adavulazidwa ndi anthu ndipo ena mpaka adaphedwa chifukwa chakudzipeleka pantchito yawo ndi malingaliro oyipa aanthu omawona apolisi ngati zirombo zaboma zogwiritsa ntchito pofuna kuthana ndi anthu.

Koma katswiri pandale Ernest Thindwa wati apolisi adadzipalira okha moto chifukwa cha momwe ankagwirira ntchito yawo m’dzina loteteza anthu ndi chuma chawo.

Iye adati kulephera kwa apolisi kudaonekera pomwe adakanika kukhazikitsa bata pakati pa anthu ochita zionetsero opanda zida zoopsa komanso mchitidwe wokondera pogwira ntchito.

“Zimachita kuonekeratu kuti a mbali yolamula akangokolana ndi anzawo, enawo ndiwo amalangidwa. Chonchi anthu n’kumati chiyani? N’chifukwa chake ubale udasokonekera ndiye akupadziwa pomwe padalakwika tingopemphera kuti akonzepo m’chaka chatsopanochi,” adatero Thindwa.

Mmodzi mwa akuluakulu a zamaufulu Timothy Mtambo watsutsa kuti Amalawi adali ndi mtopola mchaka cha 2019 ndipo wati Amalawiwo amafuna kuteteza ufulu wawo womwe boma pogwiritsa ntchito apolisi amafuna kupondereza.

“Zimenezo ndidakana ndipo ndidzakanabe. Amalawi alibe vuto koma boma pogwiritsa ntchito apolisi ndiwo adakolezera moto kuti dziko lidzadze utsi chonchija,” adatero Mtambo.

Mwa zowawa zina, Mwapasa adati apolisi ambiri adamenyedwa, nyumba zawo kutenthedwa komanso mawofesi ambiri a polisi adatenthedwa ndipo apolisi adasamuka mmalo ena momwe zinthu zidafika poyipitsitsa.

Koma Mwapasa walonjeza kuti panyengo yomwe Amalawi akhale akudikirira chigamulo cha mlandu wa zisankho, nthawi yolengeza chigamulo ndi m’masiku otsatira, apolisi apereka chitetezo chokwanira.

“N’zachidziwikire kuti anthu mitima ili m’mwamba ndipo chilichonse chikhoza kuchitika. Ife apolisi ndife okonzeka kuteteza anthu ndi katundu koma tikupempha atsogoleri ambali zonse zokhudzidwa pamlanduwo kuti mlandu uliwonse opambana amakhala mmodzi basi,” adatero Mwapasa.

Muuthenga wake wotsanzikana ndi 2019, Mwapasa adati polisi idachita bwino mbali zina monga kuchepetsa ngozi zapamsewu kuchoka pa 996 mu 2018 kufika pa 975 mu 2019.

Pangozizo, iye wati chiwerengero cha anthu omwalira chidatsikanso kuchoka pa 1163 mu 2018 kufika pa 1141 mu 2019 ndipo adati zambiri mwangozizo zidachitika chifukwa chakusasamala kwa oyendetsa galimoto ndi ena ogwiritsa ntchito msewu.

Share This Post

Powered by