Ayesa zida za Ebola
Patangodutsa sabata zitatu munthu wina wa m’boma la Karonga ataganiziridwa kuti ali ndi Ebola, aboma ayamba kuyesa zida zothandiza odwala matendawa.
Munthuyu adamwalira patangodutsa masiku ochepa chimugonekereni pa chipatala cha Karonga. Achipatala adatsimikiza kuti ngakhale amaonetsa zizindikiro za Ebola adamwalira ndi nthenda ina osati Ebola.
Koma madzulo a Lachiwiri a za umoyo kuchokera ku Lilongwe adali pa malire a dziko lino ndi Tanzania otchedwa Ilomba kukayesa zida zawo ngati bomali lakonzekera matendawa.
Malinga ndi ena mwa anthu omwe adaona izi zikuchitika akuti munthu yemwe adamugwiritsa ntchito poyesa zidazi, amasanza magazi, kutentha thupi komanso kutsekula m’mimba.
Izi zidapatsa mantha anthu ogwira ntchito pamalopo ndipo wa zaumoyo adaimbira lamya a chipatala cha Chitipa kudzamutenga munthuyu madzulo a Lachiwiri.
Munthuyu adatinso achipatala atafika pamalowa adapopera mankhwala pa malo ozungulira pa maliropo ndipo adaletsanso anthu ogwira ntchito pamalopo kuti pasaphikidwe.
Izitu zimachitika pa nthawi yomwe nawo a chipatala cha Chitipa ngakhale a bwanankubwa a bomali samadziwa kanthu kuti kuli ntchito yongoyeselera motero.
Bwanankubwa wa boma la Chitipa Humphreys Gondwe adatsimikiza za nkhaniyi.
Naye Gondwe adadziwira pa zokambirana zodziwitsana kuti ntchitoyi ikuyenda bwanji kuti aboma kuchokera mzinda wa Lilongwe amangowayesa kuti awone m’mene akonzekera.
Ndipo kalata yomwe unduna wa zaumoyo idatulutsa Lachiwiri pa November 5 idati ntchitoyi igwiridwa m’maboma a Chitipa ndi Karonga.
Kalatayo idatinso dziko la Malawi pamodzi ndi maiko ena ozungulira dziko la Democratic Republic of Congo(DRC) komwe Ebola yamanga nthenje ali pa chiopsezo cha matendawa.
“Choncho tikudziwitsa anthu kuti unduna wa za umoyo ukugwira ntchito yoyesa kukonzekera kwathu polimbana ndi Ebola,” idatero kalatayi.
Kalatayo idatinso mwa zolinga zina za ntchitoyi ndikulimbikitsa mabomawa momwe angachitire atakumana ndi munthu woganiziridwa kudwala nthenda ya Ebola, komanso kuona mavuto omwe alipo pakadali pano.
Komatu ntchitoyi idapatsa thengeneng’e anthu ambiri maka omwe amapanga bizinesi yopita ku Tunduma kudzera pa malire a Ilomba.