Nkhani

Azengedwa mlandu wopha mkazi wake ku mangalande

Listen to this article

Nyuzipepala zikuluzikulu za ku Mangalande Lachisanu zidadzala ndi nkhani ya bambo wina wa ku Malawi amene akumuganizira kuti adabaya ndi kupha mkazi wake ku Northampton.

Nkhani yoti Phillip Dafter, wa zaka 32, adabaya mkazi wake Diana wa zaka 36 ka 17 atasemphana m’banja, idayala nthenje m’nyuzipepala zazikulu ku UK monga The Sun, Daily Mail ndi The Telegraph. Dafter akumuganizira kuti adapha mkazi wakeyo mu October chaka chatha.

Chithunzi cha awiriwo chimene Diana adaika pa tsamba lake la mchezo pa 14 January 2022

Mlanduwo ukuzengedwa kubwalo la Northampton Crown Court momwe zidamveka kuti awiriwo adakumana ku UK komweko ndipo adayamba kukhalira limodzi monga banja.

Nyuzipepa ya The Sun idati wozenga milandu a Gordon Aspen adati ngakhale zinkaoneka kunjaku kuti banjalo lili pa mtambasale, zinthu sizimayenda.

“Palibe amene amazindikira kuti zinthu zidasololobana. Koma pakati pa awiriwo zinthu sizimayenda,” iwo adauza bwalo.

Malinga ndi Daily Mail, awiriwo adakangana pa nkhani zokhudza msonkho wa galimoto yawo komanso kuti Phillip amatumizirana mauthenga a Chikondi ndi mkazi wina yemwe anali ku Malawi kuno.

“Makamera a CCTV adatola kanema wa iye akukagula mipeni ya kukitchini m’sitolo ina. Adabwerera kunyumba ndipo atalasa mkaziyo ka 17, iye adamwa mowa wa whisky n’kudzibaya pamimba. Apa adapita kukakwera sitima ulendo wa ku Euston kumene adagwidwa,” idatero nyuzipepalayo.

Iyo idapitiriza kunena kuti asanakwere sitimayo adauza wogulitsa matikiti kuti: “Ndine munthu woipitsitsa.”

Ndipo ali m’sitimayo adatumiza uthenga pagulu lina la WhatsApp pomwe adati: “Boys and D. Ndikupita kundende, ndapha Diana Dafter lero.”

Phillip, yemwe adali msilikali wa nkhondo wa dziko la Britain asadapume n’kukhala woyendetsa basi. Iye adamenyapo nkhondo ku Afghanstan kumene ena amadwala matenda a kuganiza akabwerako.

Iye akukana kuti adapha munthu mwadala, koma zidachitika mwa ngozi.

Umboni wa a nyumba zoyandikira komanso komwe Phillip adakagula mipeni udaonetsa kuti patsiku Lachisanu limene izi zidachitika, Phillip amaoneka wachimwemwe momwe amakhalira nthawi zonse.

Mu umboni wina umene udaperekedwa, Phillip adauza kadaulo wa za matenda a kaganizidwe kuti ankadziwa kuti adapha mkazi wake koma adati adachita izi chifukwa Diana amamukhambitsa. “Kuphako kudachitika pomwe ndidazingidwa ndi kusagwira kwa mutu. Zidzandizunza moyo wanga onse,” iye adauza dotoloyo.

Ndipo apolisi atamumanga, iye adakana kawiri kuti sangayankhe mafunso ndipo iwo adamutsegulira mlandu wopha munthu.

Womuimira pamlanduwo, David Nathan, wati Phillip sankadiwa zimene zimachitika chifukwa mutu siumagwira choncho sadalakwe.

Malipotiwo adati ngakhale Diana adabaidwa ka 17 kuphatikizapo m’zala kusonyeza kuti amadziteteza, chipatala cha Leicester Royal Family chidapeza kuti kubaya kumene kudatenga moyo wake kudali kwa pamtima.

Nthawi yomwe mlanduwo udafika apa, Phillip adali kulira ndi kupuputa misozi yake ndi kansalu.

Mlanduwo ukupitirira.

Related Articles

Back to top button