Azula mitanda kumanda

Bambo wina wa m’mudzi mwa Mikayeli, kwa Mfumu Zulu, m’boma la Mchinji walaula dziko atakazula mitanda pa mitumbira isanu chifukwa abale a malemu sadamalize kupereka ngongole ya mabokosi omwe adatenga kwa mkuluyo.

Mneneri wa apolisi m’bomalo Kaitano Lubrino watsimikiza za nkhaniyo ndipo wati apolisiwa adamanga Robert Phiri wa zaka 21 pamlandu wopezeka kumanda ndi kusakaza zinthu.

Lubrino adati malinga ndi banja limodzi lokhudzidwa la Alfonso Sankhani wa zaka 60 wa m’mudzi omwewo, Phiri yemwe amagwira ntchito yokhoma mabokosi, adakongoza banjalo mabokosi awiri.

“Banjalo lidaperekako ndalama pang’ono za mabokosiwo, ndipo adalonjeza kuti zinazo adzamalizabe,” adatero Lubrino.

Iye adatinso koma pa 21 mwezi uno, Phiri adapita kumanda a m’mudziwo komwe adakachotsa mitanda pamitumbira isanuyo kuphatikiza ya Sankhani ndi kupita nayo kwa mabanja ofedwawo.

“Uku adawaonetsa mitandayo n’kuwauza kuti amubwenzere ndalama zake zomwe zidatsalazo,” adatero Lubrino. Pakadalipano Phiri ali kupolisi ya Kamwendo podikira kukaonekera kubwalo la milandu.

Share This Post

Powered by