Nkhani

Bajeti yafika K2.84 thriliyoni

Nduna ya zachuma a Sosten Gwengwe dzulo yalengeza bajeti ya 2022 mpaka 2023 yokwana K2.84 thriliyoni ndipo ati bajetiyo yapangidwa polingalira miyoyo ya anthu akumudzi.

Polankhula ndi Tamvani bajetiyo itangolengezedwa, kazembe wa dziko la mangalande a David Beer adati bajetiyo ndi yabwino koma zitengera kuti yayendetsedwa motani.

A Gwengwe kufika kuti akapereke bajeti

“Ndaonamo kuti boma likufunitsitsa kuchepetsa ngongole zake komanso kutukula miyoyo ya Amalawi m’njira zosiyanasiyana koma nkhani imakhala poti zimenezi zitheka bwanji,” adatero a Beer.

Mwa zina zofuna kutukulira miyoyo a anthu, a Gwengwe ati boma lachotsa msonkho pa madzi a m’mipopi ndi mafuta ophikira kuti nawo makampani opanga zinthuzi atsitse mitengo.

“Ndi chiyembekezo chathu kuti makampani opanga mafuta komanso osefa ndi kugawa madzi atsitsa mitengo chifukwa ankadandaula za misonkho pokwenza mitengo,” adatero a Gwengwe

Iwo adatinso boma lachotsa msonkho pa zipangizo za magetsi a dzuwa kuti Amalawi ambiri azitha kukwanitsa kugula kuti azikhala m’magetsi ndi kugwiritsa ntchito zipangizo za magetsi.

Bajetiyo yachepetsanso msonkho omwe alimi amadulidwa pa ndalama akagulitsa fodya wawo komanso misonkho ya Value Added Tax (VAT) yatsitsidwa m’magawo a makampani osiyanasiyana.

“Cholinga chathu tikufuna kuti makampani ang’onoang’ono komanso makopaletivi ayambe kupindula komanso akuze ntchito zawo,” adatero a Gwengwe polengeza bajetiyo.

Pa kagawidwe ka ndalama m’maunduna akuluakulu, unduna wa zamaphunziro ndiwo walandira pakulamtanda wa K462.24 biliyoni kuchoka pa K327.3 biliyoni m’bajeti ya chaka chatha.

Koma kadaulo pa zamaphunziro a Limbani Nsapato ati ngakhale ndalamayo ikuoneka yaikulu m’maso, yatsika kwambiri ikagawidwa m’nthambi zosiyanasiyana.

“M’bajeti ya chaka chatha ya K1.990 thriliyoni, undunawo udalandira K327.3 biliyoni koma pano m’bajeti ya K2.84 thriliyoni, walandira K462.24. Mukasanthula mofatsa, ndalamazo zatsika kwambiri,” adatero a Nsapato.

Iwo adati unduna wa zamaphunziro uli ndi magawo ambiri ofunika kukonza monga mabuloko a sukulu omwe agwa ndi mvula komanso mphepo chaka chino, kuonjezera aphunzitsi, kukwaniritsa masomphenya a sukulu yokakamiza ndi zina.

Unduna wa zamalimidwe wabwera pachiwiri ndi ndalama zokwana K447.66 kuchoka pa K284.4 chaka chatha koma anduna sadanene ndalama zomwe zapita ku zipangizo zotsika mtengo mwa ndalamazo ngakhale bajeti ya chaka chatha idasonyeza kuti (AIP) idalandira K142 biliyoni yopindulira alimi 3.5 miliyoni.

“Boma ndi lokondwa kulengeza kuti pulogalamu ya AIP iliponso chaka chino koma poti idakumana ndi zovuta zambiri, ikuunikidwa kuti tingatsate ziti kuti ipindule,” adatero a Gwengwe.

Koma m’nyumbayo, nduna ya zamalimidwe a Lobin Lowe adati undunawo ukufuna kusesa maina ena makamaka omwe adagulitsa ziphaso ndi makuponi awo kwa mavenda chifukwa adaonetsa kuti safuna fetereza ndi mbewu.

Koma pouzira chilonda, a Gwengwe ati m’bajetiyo boma lapereka K12 biliyoni ku Admarc ndi National Food Reserve Agency (NFRA) yogulira chimanga alimi akayamba kukolola.

Izi zagwirizana ndi maganizo omwe adapereka kadaulo pa zamalimidwe a Tamani Nkhono Mvula kuti boma lizipereka msanga ndalama zogulira chimanga ku Admarc ndi NFRA kuti aziyamba kugula chimanga alimi akangoyamba kukolola.

Unduna wa zaumoyo walandira K283.57 biliyoni kuchoka pa K187.2 biliyoni chaka chatha pomwe unduna wa zamtengatenga, mtokoma ndi zomangamanga walandira K211.74 biliyoni kuchoka pa K208.4 biliyoni chaka chatha.

Aphungu ambali zonse m’Nyumba ya Malamulo adadzuka n’kusekerera uku akuomba m’manja a Gwengwe atalengeza kuti boma lakwenza ndalama zachitukuko za Constituency Development Fund (CDF) kuchoka pa K40 miliyoni kufika pa K100 pa chaka kwa phungu aliyense. n

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button