Nkhani

Chakwera alamula kafukufuku za mayeso

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera walamula bungwe loona za mayeso la Malawi National Examinations Board (Maneb) kuti lifufuze chomwe chidachitika kuti mayeso a Fomu 4 apezeke paliponse masiku olemba mayesowo asanafike.

Unduna wa maphunziro mogwirizana ndi Maneb Lachitatu udalengeza kuti mayeso amene ana amalemba aimikidwe kaye ndipo adzalembedwenso mwezi wa March chaka cha mawa kaamba ka kubedwa kwa mayesowo.

Chakwera: Mufufuze pasanathe sabata imodzi

Koma Chakwera adati mayesowo alembedwenso usanafike mwezi wa January.

“Mufufuze pasanathe sabata imodzi ndipo amene adachititsa kuti mayeso abedwe chotere. Komanso muyenera kufufuza bwino akuluakulu a bungweli ndipo amene adalakwa ayenera kuchotsedwa kapena kupatsidwa chilango,” adatero Chakwera.

Iye adatinso akuluakulu a bungwelo ayenera kuimikidwa ntchito.

M’mawu ake, mtsogoleri wa dziko linoyo adati kusapereka chilango kumachititsa kuti adindo ena m’boma azinyalanyaza. “Taonani bwalo la milandu lidapeza kuti bungwe la Malawi Electoral Commission [MEC] silidayendetse bwino chisankho koma mpaka lero omwe adasokoneza chisankhocho akadagwira ntchito ndipo palibe amene adawachotsa kapena kuwatengera kukhoti. Izi zithe ndipo amene adasokoneza mayeso ayenera kulandira chilango choyenera,” adatero iye.

Mkulu wa bungwe loona za mavuto amene aphunzitsi amakumana nawo la Teachers Union of Malawi (TUM) Charles Kumchenga adakhumudwa ndi kuimika kwa mayesowo chifukwa zidzetsa ntchito yaikulu kwa aphunzitsi.

“Aphunzitsi tikhala pantchito yaikulu polingalira kuti ana amene ali Fomu 3 nawo akuyembekezera kulowanso kalasi ya mayeso. Boma liyenera kukhazikitsa masiku abwino kuti aphunzitsi asasokonekere kwambiri,” adatero iye.

Katswiri pa zamaphunziro Steve Sharra adati pakufunika kuti pakhale bungwe loima pa lokha kuti lithandize pantchito yofufuza chomwe chapangitsa kuti mayeso abedwe komanso kuti lisanje ndondomeko zoti mayeso asamaberedwe.

“Si koyamba mayeso kuimikidwa chifukwa m’chaka cha 2007 adaimikidwanso chifukwa adalowa chisawawa ndipo mu 2012 boma lidayamba ndondomeko zodziwitsa anthu kufunika kwa kuteteza mayeso kuti asabedwe koma chaka chino izi sizidachitike kaamba ka mlili wa Covid-19,” adatero Sharra.

Iye adati kutseka maofesi omwe amagwira ntchito zoyang’anira mayeso kaamba ka Covid-19 kukhonza kukha njira mwa imodzi yomwe yathandizira kuti mayeso aberedwe.

Nduna ya maphunziro a Agness NyaLonje idalamula kuti mayeso ayambe ayimikidwa kufikira pa 9 March 2021 ndipo kuti boma likonza ndondomeko zatsopano zodalilika.

“Boma lifunika kuti lipeze ndalama zokwana K4.5 billion yoyendetsera mayeso m’chaka cha 2021,” adatero Nyalonje.

Mkulu wa bungwe la Civil Society Education Coalition (CSEC) Benadicto Kondowe adati zomwe zachitikazi ndi chitsimikizo choti ogwira ntchito ku Maneb atayilira.

“Asanamizire kuti chitetezo chinali chopelewera chifukwa mikumano yomwe imachitika pomwe sukulu zinatsekedwa kaamba ka mlili was Covid-19 akhala akutsikimiza kuti chitetezo chilipo chokwanila,” adatero Kondowe.

Iye adati pakufunika kuti ogwira ntchito ku bungweli ayambe ayimikidwa pa ntchito kuti afufuzidwe ndipo yense okhudzidwa lamulo liyenera kugwira ntchito.

Eva Nyakuipa ndi mmodzi mwa makolo omwe ana awo amalemba mayesowa adati mayesowa ayenera kulembedwa pasanathe nthawi yaitali chifukwa zingachotse chidwi cha ophunzira.

“Tisaiwale kuti anawa adalephera kulemba mayeso patangotsala masiku ochepa chifukwa sukulu zidatsekedwa malinga ndi Covid-19. Izi zitilowanso m’thumba,” adatero iye.

Victor Thom, yemwe amaphunzira ku Bangwe Community Day Secondary School adati zachitikazi zimusokoneza kwambili.

“Zinditengera nthawi kuti ndiyambe kukozekeranso mayeso chifukwa ndi kachiwiri,” adatero Thom.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button