Chigodola chifalikira maboma ena
Matenda a chigodola amene adabuka m’maboma a Blantyre ndi Neno, ayamba kufalikiranso m’maboma ena, watero unduna wa zamalimidwe.
Matendawa adayambira ku Lisungwi m’boma la Neno ndi Kunthembwe ku Blantyre ndipo apezekanso mmadera a Linthipe ndi Bembeke m’boma la Dedza komanso Njolomole ku Ntcheu.
Izi zachititsa kuti undunawu uyimitse malonda a ziweto kapena nyama m’madera okhudzidwawa kapena kusamutsa ziweto kuchoka m’maderawa kupita m’madera ena poopa kuti vutoli lingafale.
Mmodzi mwa akatswiri a ziweto ku undunawu Dr Gilson Njunga wati matenda omwe adapezeka koyambirirawo, adachokera ku njati za m’nkhalango ya Majete pomwe ku Dedza ndi ku Ntcheu n’chifukwa cha kusakanikira kwa ng’ombe za m’mabomawa ndi za ku Mozambique.
“Tizilombo toyambitsa matendawa timapezeka mu njati koma izozo sizidwala. Chomwe chimachitika n’choti zikadyera dambo limodzi ndi ziweto monga ng’ombe, ziwetozo ndizo zimavutika,” adatero Njunga.
Iye adati m’nkhalango ya Majete muli njati zambiri zomwe zimapezeka ndi tiziromboti ndipo mmalo momwe zimadya, mumafikanso ziweto ngati ng’ombe za ku Neno ndi madera ena a Blantyre ndiye akuganiza kuti vutolo lidachokera kumeneko.
Njunga wati chigodolachi ndi choopsa chifukwa chimabweretsa chipere cha ziweto ndipo ngati sichidagonjetsedwe msanga, ziweto zimatha komanso nthambi zina zachuma zimakhudzidwa chifukwa malonda a nyama amayimitsidwa.
Boma laimitsadi malonda a nyama mmalo okhudzidwawa ndipo Njunga wati chiletso choterechi chikapitirira, mbiri ya dziko pa malonda a nyama imasokonekera.
“Taimitsa misika ya ziweto monga ng’ombe, mbuzi, nkhosa ndi nkhumba. Taletsanso kupha komanso kusamutsa ziweto kuchoka m’madera tatchulawa kupita madera ena,” chatero chikalata cha ku unduna wa zamalimidwe.
Chikalatachi chati anthu asade nkhawa chifukwa ntchito yopopera mankhwala ophera tizirombo toyambitsa matendawa ili mkati ndipo pali chiyembekezo choti matendawa atha posachedwa ndipo malonda a ziweto ndi nyama abwerera mchimake.
Njunga adati ng’ombe ikagwidwa ndi matendawa, imatuluka zilonda m’mapazi ndi kukamwa kotero imalephera kuyenda ndi kudya ndipo mapeto ake imafooka kenako n’kufa ngati siyidathandizidwe moyenera msanga.
Wapampando wa komiti yoona za malimidwe ku Nyumba ya Malamulo Chidanti Malunga adati unduna wa zamalimidwe ukuyenera kuchilimika polimbana ndi matendawa asdafike m’madera ambiri.
“Zakhala bwino kuti apezeka msanga asadafalikire ndiye zikatere pamafunika kuchilimika osagona. Matendawa si abwino chifukwa angasokoneze ulimi wa ziweto nthawi ochepa,” adatero Malunga.