Chilengedwe chikubwerera ku Mangochi
Sungapirire mfuu wa mbalame—wopokerezedwa bwino ngati nyimbo m’mitengo yachilengedwe m’boma la Mangochi.
Nkhalango yachilengedwe ya m’mudzi mwa Chembe m’boma la Mangochi lero ndi yankho, kutsatira ntchito za Malawi Lake Basin Programme (MLBP) yomwe yamanga chisa kumeneko.
Mahekitala atatu amene akhala mbulanda kwa zaka, lero avala pamene alimi alima mpunga wa kilombero komanso kusamala mitengo yachilengedwe.
Mlimi wachitsanzo m’deralo, Malefula Kulele akuti chikhalireni midzi ya Chembe, Mmadi, Kawinga, Batani, Kwitanda ndi ina ya mwa T/A Chowe, ntchito yawo kudali kuononga chilengedwe.
“Kubwera kwa pulogalamuyi kwasintha zinthu,” adatero iye. “Taphunzira kusamalira zachilengedwe. Kupanga njira zoti zititukule.”
Pamene pulogalamuyi imayamba, midziyi idalandira mitengo 2 100 kuti chilengedwe chibwerere. Padali pa 24 January 2014.
Sizidaphule kanthu, mitengo 1 500 idafa. Kutanthauza kuti pafupifupi K225 000 idapita m’madzi—ndalama yomwe ikadatha kugulira matumba 75 a chimanga ndi kugawira mudzi wa Batani womwe udali ndi nyumba 30.
“Mtengo umodzi panthawiyo timagula K150. Tidalibe ndalama zobwezeretsa mitengoyi,” adatero Kulele.
Loto lobweretsa nkhalango lidayamba kuyandama ndipo adayamba kusamala malowo posalola moto. Iwo adayambanso kusamala mitengo yachilengedwe yomwe imaphukira.
Lero nkhalangoyi yakunga mdima wa mitengo yachilengedwe. Mitengo ya magangaza, thombozi, tsamba, msolo, mphando, ngongomwa ndi ina yomwe yabweretsa mdima m’midziyi.
Mbalame zapeza nyumba. Tinyimbo ta njiwa, atchete, asisisi ndi apumbwa ndi tomwe tikupangitsa kuti anthu atambalale m’nkhalangoyo.
“Taponyamo ming’oma 5, anthu akubwera kudzapemphera komanso nthaka siyikukokoloka monga zimachitikira,” adatero Kalele amene akuti mitengo yachilengedwe yoposa 4 000 ndi yomwe ili m’khalangoyo.
Kalabu ya Chikondano yomwe ili ndi anthu 18 ndi yomwe ikuyang’anira nkhalangoyo.
Si nkhalango yokha, kumeneku alimi akonza malo amene amangogona kuti azilimapo mpunga.
Poonetsetsa kuti amayi akukhala ndi mphamvu pa zinthu, mayi Christina Mkwinda ndi membala wa sikimu ya Mangale yomwe ili ndi mpunga.
“Tikuyembekeza kupeza matumba 40 chaka chino,” adatero mayiyu amene gulu lake lili ndi anthu 10 ndipo amayi alipo 6.
Apa ndiye kuti gululi likuyembekeza kupha pafupifupi K2 miliyoni pa matumbawo.
“Tikufuna tigule zipangizo zokwanira komanso kukuza munda. Ndalama yake ndi imeneyi kupatula kuthana ndi mavuto athu,” adaonjeza Mkwinda.
Pologalamu ya MLBP yomwe ikuchitika m’maboma a Mangochi ndi Salima ikulimbikitsa anthu mmene angathananirane ndi mavuto omwe amadza kaamba kakusintha kwa nyengo powapatsa upangiri ndi zina.