Nkhani

‘Chilonda chatukusira mu DPP’

Bwerani poyera mulankhule kwa Amalawi. Awa ndi mawu a akadaulo pa ndale pamene alangiza mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ndi wachiwiri wake Saulos Chilima kuti alankhulepo pa mpungwepungwe omwe wabadwa m’chipanicho.

Akadaulowo, Emily Kamanga ndi Henry Chingaipe alangiza izi kutsatira kusamvana pa yemwe atengere chipanicho kuchisankho cha 2019.

Chilima ndi Mutharika

M’sabatayi, anthu akhala akubwera poyera ndi zovala za DPP zokhala ndi nkhope ya Chilima kuti ndiye atengere DPP kuchisankho cha 2019.

Koma Lolemba, mlembi wa chipanicho Grelzedar Jeffrey adatsindika kuti zovalazo si za DPP chifukwa zovala zawo zimakhala ndi nkhope ya Mutharika kapena mkulu wake Bingu yemwe adayambitsa chipanicho.

“Tikudziwa akupanga izi ndi adani athu, kotero dziwani kuti chipani chili ndi mphamvu kulanda zovala zimenezo. Zovala za DPP zimakhala ndi nkhope ya yemwe adayambitsa chipanichi Bingu wa Mutharika kapena amene ndi mtsogoleri pano,” adatero Jeffrey.

Iye adaopseza: “Titengera kukhoti aliyense amene akugawa kapena kupanga zovalazo.”

Koma mmodzi mwa anthu amene sakufuna Mutharika, Bon Kalindo wati iye pamodzi ndi gulu lawo sabwerera ndipo sachita mantha pokhapokha Chilima akhale pachiongolero.

Sabata yatha, anthu adadzidzimuka pamene adamvetsera uthenga womwe Jeffrey amalankhulana ndi nduna ya maboma ang’ono Kondwani Nankhumwa.

M’zolankhula zawo, Jeffrey adaulula kuti Chilima sakubwerera ngakhale Mutharika amulonjeza zokhalanso wachiwiri wake.

“Ineyo ndidalankhula naye [Chilima] koma adanditsimikizira kuti sakufuna kukhala wachiwiri kwa Mutharika ngakhale kumsonkhano waukulu sadzapitako ati angokhala.

“Ndinadabwa kuti basi angokhala? Ndiye ineyo ndi wandale ndikudziwa chomwe akutanthauza,” adatero iye.

“Bwana ndakhala ndikukuuzani, wamisala adaona nkhondotu. Chilichonse chimene ndakhala ndikulankhula ndi chomwe chikuchitika. Anthuwatu adayamba kale.

“Ndidakuuzani kuti Chilima sabwereranso ndipo akupanga zake. Anthu awa bomali alilowerera. Ngakhale bwana [Mutharika] atani maka Chilima salola. [Noel] Masangwi sabwereranso. Bwana aitanitse NGC, chifukwa kumsonkhano waukulu Chilima sangawine. Akulimbana ndikugawa DPP cholinga MCP itole boma,” adatero mlembiyu.

Mkamanga akuti chofunika nchoti Mutharika komanso Chilima abwere poyera ndi kulankhula kuti zonsezi zitheretu.

“Nkhani yonseyitu ikukamba za awiriwo, ndiye ngati atalankhula, zonse zingathe. Komabe ndilibe chikhulupiriro ngati awiriwo amalankhulana. Apapa zavuta basi ndipo ndikukaika ngati angamvane,” adatero Mkamanga.

Naye Chingaipe adati kusalankhula kwa awiriwo ndikomwe kukuze bala la chipanicho kotero ayenera abwere poyera.

“Komabe funso ndiloti ayankhule liti? Panopa? Nanga chichitike n’chiyani akalankhula pano? Zonse zili poti kodi akamalankhula anena chiyani?” adatero Chingaipe. n

Related Articles

Back to top button