CMST iyambanso kugawa mankhwala

Nkhokwe ya mankhwala ya Central Medical Stores Trust (CMST) yatsiriza kukambirana ndi mabungwe omwe amathandiza dziko lino pa nkhani ya zaumoyo kuti udindo wosunga ndi kugawa mankhwala ubwerere m’manja mwake.

Mkulu woyendetsa ntchito zaumoyo m’dziko muno, Dr Charles Mwansambo, komanso mkulu wa CMST, Feston Kaupa, atsimikiza za nkhaniyi.

Ngoma: Ana ndi amayi amavutika

Akuluakulu awiriwa ati izi zikutanthauza kuti mabungwe ndi maiko othandiza dziko lino pa zaumoyo akhutira ndi kusintha kwa ndondomeko zoyendetsera ntchito za ku nkhokweko makamaka pa chitetezo cha mankhwalawo.

“Apa ndiye kuti mabungwe ali ndi chikhulupiliro mu nkhokwe yathu ya mankhwala chifukwa adayamba kupereka okha mankhwala m’zipatala kusolola mankhwala kutavuta m’zaka za mu 2002,” watero Mwansambo.

Kaupa wati, mwa zina, mabungwe adatuluka mu ndondomeko yakale yodzera ku nkhokwe pogawa mankhwala pofuna kuti zinthu zina zisinthidwe ku nkhokweko ndipo zonse zatheka tsopano.

“Tidasintha zambiri monga chitetezo cha mankhwala mu nkhokwe, komanso pakagawidwe kake. Nkhokwe zathu n’zamakono, n’zovomerezeka kusungamo mankhwala, komanso tili ndi galimoto zapamwamba zokhala ndi zipangizo zoilondola kuti mankhwala asabedwe,” watero Kaupa.

Koma kadaulo wina pa zaumoyo Dorothy Ngoma wati ngakhale nkhaniyi ikumveka yokoma, akuluakulu aku nkhokweyo akuyenera kuganizira mozama amayi ndi ana pa ntchito yawo.

“Apa zikutanthauza kuti mphamvu zikubwera m’manja mwawo ndiye sitikufuna kuti posachedwapa tiyambenso kumva nkhani zogonthetsa m’khutu kuti mankhwala ena sakupezeka kapena ndiwoonongeka ayi. Zimenezi zimazunzitsa amayi ndi ana,” watero Ngoma.

Kadauloyu wati pomwe mabungwe ankaganiza zotuluka m’ndondomekoyi adaona kuti amayi ndi ana ndiwo amavutika. Choncho akhoza kukhala akuyesa ngati utsogoleri wa ku nkhokweyo wasinthadi.

“Chomwe chimavuta n’choti amakhalapo ena ofunadi kusintha zinthu, koma mkati momwemo mukhalanso ena atambwali ndiye tiyeni tiona kuti aziyendetsa motani, koma langizo langa ndiloti tichepetse mtima wodzikonda,” watero Ngoma.

Mwansambo wati mabungwe atakhumudwa ndi kubedwa kwa mankhwala,

adanyanyala n’kuyamba kupereka okha mankhwala m’zipatala moti kuchoka 2002, kudali magulu oposa 12 osunga ndi kugawa mankhwala okha.

“Chomwe chimachitika n’choti padali ena osunga ndikugawa mankhwala okhudzana ndi matenda a edzi, ena amapanga za mankhwala achifuwa chachikulu, ena zauchembere ndi zina zosiyanasiyana, koma tsopano zonsezi zibwera pamodzi pansi pa nkhokwe yathu,” watero Mwansambo.

Iye wati izi zithandiza kuchepetsa ndalama zonyamulira mankhwala kupita m’zipatala za boma chifukwa ofesi ya zaumoyo ikayitanitsa mankhwala, onse azinyamulidwa pakamodzi m’malo moti ena apititse pa wokha, enanso pa wokha.

Kaupa wati panopa, akuluakulu akukonza ndondomeko yoti pakhale njira yoti mabungwe onse azitha kulondoloza momwe mankhwalawo aziyendera akafika ku nkhokwe, komanso akatuluka ulendo wa ku zipatala za m’maboma. n

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.