Nkhani

‘Dekhani za a bushiri’

Oimira anthu pa milandu, a Jai Banda komanso a Khwima Mchizi apempha Amalawi kuti adekhe pa mlandu omwe mneneri wa mpingo wa The Jesus Nation a Shepherd Bushiri komanso akazi awo a Mary Bushiri akuzengedwa.

Iwo amathirira ndemanga pa chikalata chomwe bungwe la Maseko Ngoni Heritage Trust yalembera mlangizi wamkulu wa boma pa milandu a Thabo Chakaka Nyirenda yomwe ikupempha boma kuti lisawatumize awiwira m’dziko la South Africa kuti akayankhe ina mwa milandu yomwe akuwaganizira.

A Bushiri ndi akazi awo mmbuyomu

Izi zikudza bwalo la milandu mu mzinda wa Lilongwe litagamula kuti awiriwo awatumize ku South Africa kumene adathawa belo ali pa milandu yokhudza kuzembetsa ndalama ndi ina.

Ndipo magulu osiyanasiyana kuphatikiza azipembezo zina akhala akupempha boma kuti lilowererepo kuti a Bushiri ndi akazi awo asatumizidwe ku South Africa ponena kuti awiriwa ndi nzika za Malawi ndipo akuyenera kuti dziko liwateteze.

Malingana ndi kalata yomwe adasainira ndi mlembi wankulu wa bungwe la Maseko Ngoni Heritage Trust impi Kandi Padambo Ndau, iwo afotokoza kuti awiriwa asatumizidwe ku Joni pofuna kuwateteza komanso kuti alandire chilango choyenera pa milanduyi.

“Kuwatumiza a Shepherd Bushiri komanso akazi awo a Mary Bushiri kuli ndi kuthekera kopsinja chilungamo. Timakhulupirira chilungamo pa nkhani za malamulo komanso kulemekeza mapangano omwe dziko la Malawi lidalowa ndi maiko ena kuti nzika za dziko lino zizitha kupeza chilungamo mosavuta.

“Tikukhulupirira kuti kutumiza awiriwa ku South Africa kuli ndi kuthekera kopsinja chilungamo kwa awiriwa ndipo chifukwa cha ichi tikupempha boma kuti lisawatumize awiriwa mdziko la South Africa,” chidatero chikalatacho.

Koma poikirapo mlomo, a Banda adati ngati dziko tikuyenera kudikira kuti khoti lichita chigamizo chotani pa lokha pomwe mlanduwo walowa ku apilo.

“Tili ndi nthambi ya za chilungamo komanso nthambi ya aphungu onsewa si kuti angokhala ayi choncho ndi kuona kwabwino kuti tisiire bwalo la milandu kuti lipange chiganizo. Komanso njira ina kudali kofunika kuwathandiza ndi maganizo kwa awiriwa momwe angadzipulumutsire pa milandu yomwe akuwaganizira,” adatero a Banda.

Iwo adaonjezera kuti ngakhale a Bushiri ndi akazi awo akuchita zabwino zambiri m’dziko muno, koma chilungamo ndi chofunika kuti chilondolozedwe.

Kumbali yawo a Mchizi adati akutha kumvetsetsa zomwe maguluwa akufuna koma pakuyeneranso kuzindikira kuti palibe yemwe ali pa mwamba pa lamulo.

“Popempha kuti munthu ayankhe milandu lingaliro limakhala loti munthu athe kulandira chilungamo pofuna kumva mbali yake koma akapezekabe kuti ndi wolakwa khoti lidzawatumiza.

“Awo ndi maganizo awo ndipo ndikukhulupirira kuti akuyenera kutero chifukwa ndi ufulu wawo koma ndikuona kwabwino kuti pakufunika kusiya khothi lipange chiganizo palokha,” adatero a Mchizi.

Mlandu wa apilo wa a Bushiri ayamba kuumva pa 12 June, pomwe mneneriyo.

Sabata yatha, iwo adazizwa ndi nthambi yozenga milandu m’dzikolo litalengeza kuti ndege ya a Bushiri imene yakhala ku bwalo la ndege la Lanseria kuchokera m’chaka cha 2020 igulitsidwe pa mtengo wa 50 miliyoni rand (pafupifupi K4.4 biliyoni).

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button