Nkhani

DPP yakoka jekete la Tonse Alliance

Chipani cha Democratic Progressive (DPP) chakokera boma la Tonse Alliance ku khothi komwe chikufuna kuti liunikile ngati kusankhidwa kwa a Lazarus Chakwera ngati mtsogoleri wa dziko lino komanso a Saulos Chilima ngati wachiwiri wawo kunali kolondola.

Chipanichi chapeza mangolomera pa zomwe boma lidachita pochotsa makomishonala ena omwe mtsogoleri wachipanicho a Peter Mutharika adasankha pamene amalamulira dziko lino.

Oweruza milandu pa mlandu wa chisankho chaka chatha amatetezedwa ndi asilikari

Apa, chipani cha DPP chamanga mfundo yoti makomishonala omwe sadali ololedwa kuyendetsa chisankhowo ndiwo adayendetsa chisankho chobwereza cha mu June 2020 chomwe a Chakwera ndi a Chilima adalowera m’boma.

“Chomwe tikufuna n’choti khothi litanthauzile ngati n’kololedwa kuti chisankho chomwe makomishonala osaloledwa anayendetsa nchovomerezeka. Makomishonala amenewa ndiwo adayendetsa chisankho cha 2020 chomwe a Chakwera adapambana komanso adayendetsa zisankho zobwereza za aphungu ndi makhansala ena,” adatero m,modzi mwa ma loya a DPP a Samuel Tembenu.

 Koma mlangizi wa boma pa malamulo a Thabo Chakaka Nyirenda yemwe akuyimilira boma pa mlanduwo ati nfundo zonse zomwe maloya a DPP akubweretsa ku khothiko n’zopanda mchere komanso akudumpha masitepe ambiri.

Mwazina, a  Nyirenda ati maloya a DPP samayenera kupempha khothilo kuti liunike nkhaniyo chifukwa khothi lomwelo lidaunikapo kale n’kupereka chigamulo chake komanso DPP ngati chipani sichimayenera kukamang’ala chifukwa sichidayime ndiichocho pachisankho.

 “Kutengera malamulo, khothi silingaunikenso chigamulo chake chomwe choncho pempho lawo ndilozizira komanso DPP ikudzamang’ala ngati ndani? Amayenera kubwera kuno ndi a Mutharika chifukwa ndiwo adapikisana nawo pachisankho,” adatero a Nyirenda.

Iwo adapitiriza kunena kuti zomwe achita a DPP n’kufuna kuti a Mutharika apindule pa kulakwitsa kwawo komwe zomwe n’zosavomerezeka ndipo adapempha khothilo kuti lingothetsa mlanduwo chifukwa ulibe mutu weniweni.

“A DPP akufuna kuti khothi libwezeretse momwe zinthu zidaliri chisankho cha 2020 chisadachitike kutanthauza kuti a Mutharika abwerere pa utsogoleri wa dziko lino chifukwa cha kulakwitsa kwawo komwe zomwe n’zosayenera,” adatero a Nyirenda.

Koma a Tembenu, womwe adakhalapo nduna ya zamalamulo ndi chilungamo adati DPP ngati chipani ili ndi ufulu wonse wokamang’ala kukhothi ngati chipani chodziwika bwino chifukwa malamulo akuchilola kutero.

“Gawo 40 ya malamulo imapereka ufulu kwa M’malawi kapena gulu lililonse lokhudzidwa kukamang’ala kukhothi bola ngati lili ndi zifukwa zokwanira. DPP n’chipani chodziwika komanso chili ndi aphungu ambiri ku Nyumba ya Malamulo ndiye ilephelerenji kukhala ndi ufulu umenewu?” iwo adatero.

Loya winanso wa DPP a Charles Mhango adati mlanduwo ndiomveka chifukwa malamulo amalola kuti nkhani iliyonse yokhudza kuunikira malamulo ikhoza kutheka ndi majaji osaposa atatu.

Khothi la Constitutional lomwe likumva mlanduwo lili ndi majaji asanu omwe ndi a Sylveter Kalembara ngati otsogolera, a Rowland Mbvundula, a Dorothy NyaKaunda Kamanga, a Annabel Mtalimanja ndi a Thom Ligowe.

Lachinayi lapitali, a Mhango adapindanso nkhani polowetsa nfundo ina yoti a Nyirenda akuimilira boma pa mlanduwo chonsecho sadalumbilire ofesi yawo koma a Nyirenda adaunikira a Mhango kuti ofesi yawo siyilira kulumbira kuti iyambe kugwira ntchito chifukwa si ofesi ya ndale.

 Mu June 2021, woweruza milandu khothi lalikulu a Kenyatta Nyirenda, pogamula mlandu womwe mlembi wamkulu wa MCP a Eisenhower Mkaka adakasuma kuti a pulezidenti achotse makomishonala anayi omwe a Mutharika adasankha mophwanya malamulo, adapeza kuti a Mutharikawo adapotozera dala malamulo ndi cholinga choti kuti chipani chawo chikhale ndi danga lalikulu.

 A Mutharika adasankha a Jean Mathanga, a Steven Duwa, a Linda Kunje ndi a Arthur Nanthuru m’malo mosankha atatu kuti nawo a MCP omwe panthawiyo adali ovomerezeka kukhala ndi makomishona ku MEC akhale ndi atatuso.

“Zikuchita kuoneka zokha kuti makomishonalawo sadasankhidwe moyenerera,” adatero a Nyirenda.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button