Nkhani

Dziko layaka moto, Bushiri wachenjeza

Mneneri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG) Shepherd Bushiri wachenjeza atsogoleri andale kuti mpungwepungwe womwe uli m’dziko muno utha kudzetsa mavuto a akulu.

Bushiri, yemwe amakhala ku South Africa, wapempha atsogoleriwo kuti akonzekeretse anthu awo kudzavomera zotsatira za mlandu wa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino womwe uli ku khoti.

Kudali mkokemkoke ku Lilongwe Lachiwiri, anthu okwiya atatseka misewu ndi matayala a moto

Zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM zidakokera ku khoti chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) ndi bungwe la Malawi Electoral Commission powaganizira kuti adabera chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino.

Bushiri adati kupanda kukonzekeretsa anthu kudzalandira chigamulo cha khoti kutha kudzaonongetsa katundu wambiri kuposa yemwe waonongeka kale.

Zinthu zambiri zaonongeka kaamba ka zionetsero zomwe zakhala zikuchitika m’dziko muno pofuna kukakamiza wapampando wa MEC Jane Ansah kuti atule pansi udindo wake pomuganizira kuti sadayendetse bwino zisankho zapatatu za pa May 21.

Bungwe la Human Rights Defenders Coaliation (HRDC) ndilo likutsogolera zionetserozo.

Ansah adakana kutula pansi udindo wake zomwe zachititsa kuti HRDC ipitirize kuchita zionetsero.

Bushiri adati zionetserozi zaonetsa kale Amalawi mbwadza, koma zenizeni zazikulu zikubwera ngati anthu sadzavomereza zotsatira za mlanduwo.

“Anthu akutaya miyoyo. Posachedwapa mnyamata wamphamvu zake ku Karonga adataya moyo wake m’dzina la zionetsero.

“Anthu akumenyedwa n’kumasiyidwa atatsala pang’ono kufa chifukwa amachokera m’chigawo china kapena amatsatira chipani china ndipo atsogoleri athu akuoneka kuti sakufuna kugwirizana,” iye adatero.

Bushiri adati sakudana ndi zionetsero chifukwa ndi ufulu wa anthu kutero, koma chomwe akudana nacho ndi zipolowe zomwe zionetsero zikudzetsa.

Iye adati ndiwokonzeka kukhala mkhalapakati wa mbali zonse zomwe

sizikumvana pa nkhani ya chisankho cha pa May 21 2019.

Mneneri wa MCP Maurice Munthali adati za mtendere si zachilendo mu chipani chake.

Iye adati zomwe Bushiri akunena ndi zomwe mtsogoleri wa chipanicho Lazarus Chakwera amafotokozera otsatira ake.

Mneneri wa chipani cha DPP Nicholas Dausi adangoti chipani chawo ndi +cha mtendere, koma sadathirirepo ndemanga pa zomwe Bushiri adalankhula.

Related Articles

Back to top button